Amai

Katakwe

AMAI

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Chadzulo lake Katakwe adafika kunyumba kwake mochedwa komanso ataubwira kwambiri. Chidamudzutsa lidali phokoso kuchokera mnyumba yoyandikira. Kenaka adadzamva kugogoda pachitseko mwamphavu.

 

“Achimwene, tsegulani andipha ine!” mkuwe udamveka pakhomopo. Mauwo adawazindikira kuti adali a Nafe, msungwana yemwe ankakhala nyumba yoyandikira.

 

Ngakhale adali ndi matsire, mantha omwe adali mmawu a msungwanayo adamupangitsa kuti adzuke msanga. Atatsegula chitseko adapeza Nafe akulimbana ndi gulu la amai omwe adamuzungulira ngati agalu olusa. Adali atamung’ambira zovala ndipo adangotsala ndi panti yekha.

 

Katakwe adalowerera mwachangu namulanditsa msungwanayo. “Amai, chikuchitika nchiyani?”

 

“Tabwera kudzapha huleli,” adatero mai wina woumbidwa ngati mvuu kwinaku akung’amba kamisolo ya Nafe.

 

“Amai, ndinu akuluakulu. Nkhani sakamba chonchi. Vuto ndichani?”

 

Mai wonenepa uja adalavulira pansi. “Phu! Palibe zokambirana. Ife tabwera kudzathana ndi hule lodyera kumalisecheli. Lero tiliyendetsa mbulanda liyaluke.”

 

Katakwe adakweza manja ake. “Ndati tafotokozani kuti dandaulo lanu ndichani?”

 

“Hule ili lakhala likusokoneza banja lamzathu,” mvuu ija idayankha. “Poyamba timangova kuti mwamunayo ali ndi chibwenzi. Titafufuza tapeza kuti ndi iyeyu. Ndiye inu musalowerere. Galuyu tithana naye.”

 

Katakwe adatembenukira kwa Nafe. “Kodi nkhani yake ndiyotani?”

 

“Achimwene, monga mukudziwa ndili pachibwenzi ndi James. Paja amabwera ngakhale kudzagona pakhomo panga,” adalongosola Nafe. “Ndiye lero ndangodabwa amaiwa akukhamukira pakhomo panga nkuyamba kundimenya ali ndikusokoneza banja la mzawo.”

 

“Kumene. Hule limeneli likusokoneza banja langa,” msungwana yemwe mwachidziwikire kuti adali mkazi wa James adatero.

 

“Amai, James akunenedwayo ndikumudziwa ndipo ndimacheza naye. Chomwe adafotokoza atafika pano chidali chakuti banja lake lidatha,” Katakwe adaunikira “Zoti ali ndi mkazi, Nafe samadziwa.”

 

“Amadziwa; ndi bitchi ameneyu!” amai aja adakuwa.

 

“Uhule wake uli pati? Ngati pali hule ndi mwamuna wanuyo. Nafe sadachoke pano kukafunsira mwamuna wanu,” Katakwe adaika chilungamo pambalanganda. “Zimenezi amai mumazikonda. Mukamva mwamuna wanu ali ndi chibwenzi mumakalimbana ndi mkazi winayo. Bwanji osalimbana ndi mwamuna wanuyo yemwe amakaputa dala mkazi wina akudziwa kuti ali ndi banja?”

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

6 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *