Chithandizo Cholakwika

Katakwe
CHITHANDIZO CHOLAKWIKA
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Mumzinda wa Blantyre adali mlaliki wamphamvu ndipo adali ndi utumiki wakewake. Tsikulo adali atakwapatira baibulo paulendo wokalalikira ku Makhetha.

“Thandizeni, abusa,” mawu adamveka kumbuyo kwake mopolokozana ngati kwaya akudutsa mu Limbe. Potembenuka adaona kuti ankapemphawo adali ana amasikini okwana asanu.

Katakwe sadasamale, adapitirira kuyenda. Ana aja sadagonje, adamutsatira ngati anapiye akamatsatira mawo.

“Aaaa, bwererani-mukutani kumapempha m’tauni muno?” Katakwe adafunsa mwaukali. “Go back,” iye adatero akuwabweza ana aja ndi baibulo lake.

“Abusa, ndiyetu mwaonjeza,” mkulu wina adatero.

“Ndaonjeza? Bwanji?” Katakwe adafunsa.

Mkuluyo adamwetulira. “Ndakhala ndikutsatira maulaliki anu, munthu wa Mulungu. Mumakonda kunena kuti tizithandiza anthu ovutika.”

“Zoona,” adavomereza Katakwe.

“Ndiye zomwe mukuchita apazi zikusemphana ndi chiphunzitso chanu,” adaunikira mkuluyo.

Katakwe amuyang’anitsitsa mkuluyo. “Motani?”

Mkuluyo adamugenda Katakwe ndi diso lodabwa. “Moti simukuona kuti anawa ndi ovutika?”

“Ndikuona,” Katakwe adatero akumwetulira. “Koma kuthandiza ana ovutika sikuwapatsa ndalama mumsewu.”

“Mukutanthauza chiani?”

“Anawa ndikhoza kuwapatsa ndalama lero, koma nanga mawa? Kuthandiza ana opempha nkuwapezera chochita chomwe chikhoza kuwachotsa mumsewu monga kukawasunga kunyumba zosunga ana opempha mumsewu komwe akhoza kukaphunzira sukulu nkudzakhala nzika zodalilika.”

“Kuwapititsa kunyumba zimene zija amakathawako,” mkulu uja adatero.

“Mukudziwa chomwe amakathawirako? Nchifukwa cha anthu ngati inu omwe mumawapatsa ndalama akakupemphani. Tonse titapanda kuwapatsa ndalama akatipempha, angakhalenso mumsewu?”

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *