Katakwe Pa Nyuwele

Katakwe

Panyuwele

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

“Mmoyo wanga, Katakwe adatero. Mmoyo wanga, sindidalowepo chaka chatsopano monjoya chomwechi!”

 

Belita adamusisita Katakwe pachifuwa. Nawenso nthabwala! Tsono ukuti mkazi wako unamuyimba yotani?

 

Ndimakuuza amene uja ndi kape. Komanso kuti ndibwere naye kunyanja kuno ndiye adzavale mwado ngati momwe wapangira iwemu ana akhoza kuthawa pomayesa ndi mvuwu, Katakwe adatafula. “Mkazi wa pakhomo ndi chigayo. Tikazika pakhomo, yake ndi yogaya ana.

 

Onse adaseka mowonetsa kumva kukoma. Awiriwa ankacheza pamchenga ku Salima. Udali mmawa wa tsiku loti angolowa kumene chaka chatsopano. Katakwe adali gada, atatsinzina. Iye adangovala kabudula yekha. Belita adagona chopingasa chafufumimba, atatsamira mutu wake pachifuwa cha Katakwe ngati pilo.

 

Awiriwo adali atafika kunyanjako chadzulo lake kudzatsanzikana ndi chaka komanso kudzanjoya kuti alowa m’chaka chatsopano. Iwo adali atachezera ndi kunjoya. Ndipo tsopano ankapitidwa kamphepo kayaziyazi m’mbali mwanyanjamo.

 

Darling, kumuzemba mkazi pa nyuwele sipano, adaumirira Belita. Ukuti wamudyetsa njomba yotani?

 

Nkhope ya Katakwe idawala. Pulani yake inali yosavuta. Ineyo ndinakonza kakhadi kapamwamba kowonetsa kuti andiyitana kuphwando lina lake la amuna okhaokha ku Blantyre lomwe lidzachitike pa nyuwele.

 

Ndiye?

 

Basi nkhani inathera pomwepo. Mzimayi n’kupita ku phwando la amuna okhaokha?

 

Asi.

 

Eeetu, iye samadziwa kuti njophera awemba. Ndangochoka apo ndimuja ndimadzakutenga ku Kawale ife nkumabwera wa kunyanja kuno, adatero Katakwe.

 

Moti mkazi wako akungoti uli ku Blantyre?

 

Funsoli sadathe kuliyankha malinga n’kuti adangozindikira mwana wake woyamba wadzagwa pakati pa iye ndi Belita. Akuti nchiyani, mwana wake wachiwiri adadzagona mbali inayi. Adakati kodi ndikulota, mwana wake womaliza adadzamugonera pamimba.

 

Adadi! What a a nice surprise. Amamitu amayesa mwapita ku Blantyre ndiye ife tinawaumiriza kuti abwere nafe kunyanja kuno, anawo adatero mwachisangalalo. Suuyu takupezani. Happy New Year, daddy!

 

Adaona mkazi wake akubwera. Ana adakathawadi. Komatu samaoneka ngati mvuu. Amaoneka ngati chipembere. Chipembere chake cholusa moipa!

 

End

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *