Katakwe Nkhani ya Chikondi

 

Katakwe

Nkhani ya Chikondi

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Nthawi yomwe Katakwe ankafika pakhomo pa Likisho, adamuona mzakeyo akulowera kuseri kwa nyumba. Pozungulira khumbilo, Katakwe adadzidzimuka kumuona Likisho akuponya chingwe mumtengo.

 

“Chikatere?” Katakwe adafunsa mozizwa.

 

Likisho adatembenuka modabwa, chingwe chija chidakali m’manja. Sadayankhe nthawi yomweyo. Kwa kanthawi adakhala akupukusa mutu.

 

“N’chiyani, bwanawe?” Katakwe adafunsa akumugwira mzakeyo paphewa momulimbikitsa.

 

“Aise ine ndaona kuti kuli bwino ndife,” Likisho adayankha. “Chokhalira moyo sindikuchiona.”

 

Katakwe adamulannda chingwe chija. “Tiye mnyumba ukandifotokozere.”

 

“Aise, ukudziwa kuti ndakhala paulova kwa nthawi yaitali. Ukudziwa ndili pantchito banja langa limayenda bwino. Zinthu zidayamba kusokonera kuyambira nthawi ija adandichotsa ntchito,” Likisho adatero tsozi lili mbwe atalowa mnyumba.

 

“Ndikudziwa,” adavomereza Katakwe.

 

“Dzulotu basi mpomwe alamu ako alongedza katundu wawo ali sangakhale ndi mwamuna wa manja lende,” adatsendera Likisho.

 

Mmalo momumvera chisoni mzakeyo, Katakwe adaseka. “Ukusekanso? Sukuona mzako ndili pamoto?”

 

“Aise, chomwe ndikuseka n’chakuti ukudabwa kuti mkazi wako wakuthawa. Chodabwitsa n’chiyani pamenepa?”

 

“Iye uja tidamanga ukwati wa kutchalitchi…tidalonjezana kuti tidzakhalira limodzi pamavuto ndi pamtendere…”

 

Katakwe adaseka. “Mawu amene aja ankachoka mumtima mwake kapeana amangobwereza zomwe abusa ankanena?”

 

“Aise, sindikumvetsa…”

 

“Chomwe ndikufuna kufotokoza n’chakuti mwamuna ngati sungakwanitse kusamala mkazi yembekeza kuti banja limenelo litha,” Katakwe adatero. “Mwamuna woti sangasamale mkazi azitani naye mkaziyo?”

 

“Azikhalira chikondi…?”

 

Katakwe adaomba mmanja. “Chikondi? Chikondi n’chani? Pali chinthu choti ukhoza kuloza kuti ichi ndi chikondi?”

 

Likisho sadayankhe.

 

“Chikondi pachokha kulibe. Mkazi akati amakukonda ndiye kuti amakonda china chake pa iweyo. Ngati chinthu chimenecho chichoke, chikondinso chimachoka.”

 

“Katakwe…”

 

“Monga iweyo mkazi wako adaakonda ndalama zomwe udali nazo koma poti ndalamazo zidali ndi iwe nchaka ankati amakukonda,” Katakwe adaunikira. “Ndalama zachoka, akondanso chani pa iwe?”

 

“Komabe chikondi chilipo…”

 

Katakwe adaimika dzanja. “Pachokha chikondi palibe. Olo panopa utati ungopeza ntchito mkazi wako wathawayo akhoza kubwerera chifukwa sikuti wachoka chifukwa amadana nawe koma panopa ulibe zomwe zimamupangitsa kuti akukonde. Paja ndidakuperekeza kokafunsa mbeta. Kodi titafika funso loyamba makolo ake lidali loti chani?”

 

“Ndimatani?” Likisho adayankha mwachangu.

 

“Tsiku limene lija udakayankha kuti ndimangokhala, makolo ake adakakulola kuti umukwatire mwana wawoyo?”

 

“Ayi.”

 

“Adakulola chifukwa udali ndichochita choti ukhoza kusamala mwana wawo,” Katakwe adakhadzula. “Lero ulibe chochita, umati mwana wawoyo azitani pakhomo pano?”

 

Likisho adasowa choyankha.

 

“Eetu. Amuna zikativuta tizingokonzekeratu kuti banja livuta; osachedwanso n’kudzimangilira. Kumangolimbiratu mtima kuti nthawi iliyonse bandi igawana zida,” adalangiza Katakwe. “Tiye apa tikautibule. Ukadzapeza ntchito udzapeza mkazi wina olo yemwe wathawayu uona adzabweranso. Ndi mmene moyo ulili.”

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

12 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *