Katakwe Ngombe Yaponda Thope Yamwa

Katakwe
Ngombe Yaponda Thope Yamwa
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Mavalidwe a chitenje a amayi amaonetsa mmene zinthu zilili panthawiyo. Akamangira mchiuno mwenimweni ndiye kuti palibe chabwino kapena choipa. Akamangira mmunsi mwa chiuno ndiye kuti ali mchikondi. Akangomangira mkhwapa nde kuti zinthu sizili bwino.

Mmene Katakwe amatulukira pakhomo pake nthawi idali itadutsa pakati pa usiku. Adamupeza mkazi wake akumudikira pa balaza chitenje atamangira mmawere, manja atapingasa pachifuwa, nkhope ataipitsa ngati yagalu wofuna kulandidwa fupa lonona.

Nthawi ino mukuchokera kuti? mwana wamkazi adafunsa.

Funsoli lidamudabwitsa Katakwe. Mmayesa ndinakuuzani kuti ndidzera kumowa?

Mhu! mkazi wake adadzuma. Nthawi pano ndi thu koloko mbandakucha; kumowa kwake kuti kobwera mpaka nthawi ino?

Ku bala komwe ndinali.

Mwana wamkazi adaseka monyodola. Katakwe, Im not stupid. Unali kuchibwenzi. Kumowa kwanji kofika mpaka nthawi ino?

Komwe ndinaliko

Sizingatheke. Munthu wabwinobwino sangakhale kumowa mpaka kudutsa midnight. Ndakuuza Im not stupid, Katakwe. Unali ku chibwenzi.

Katakwe adadya mutu. Adakumbukira kuti nkhani yamunda amakambira pamunda pomwepo. Kenaka adamugwira dzanja mkazi wakeyo. Mayi, tiyeni kuno. Munthu wamayi momwe ankati nchiyani adali atamukokera kugalimoto, ulendo nkupsa.

“Nkhani yamunda amakambira pamunda pomwepo, Katakwe adayankha poponya mwambi.

Adatulukira pamalo pomwe padali mabalapo. Magetsi adali ngwe ngati masana. Zoyimbira zinkabandula nyimbo ngati kuti anthu adali pamenepo adali ogontha mkutu. Anthu adali laka ngati pamsika.

Waona azibambo onse ali panowa? Azikazi awo akuganiza kuti ali ku zibwenzi kapena kumahule; kuno nkuzibwenzi? adafunsa Katakwe.

Ayi.

Vuto azimayi mumangoti amuna anu akachedwa kumowa mwati ali kuzibwenzi kapena kumahule. Zotsatira zake mumangodzikweza ma BP mmalo moti muzigona.

Komabe munthu woti uli ndi banja

Make mwana, make mwana! Mwamuona mkulu uyo? Ngwamkulu kuposa ine, ali ndi mkazi, ana komanso zidzukulu, adatero Katakwe akuloza mkulu wina wadazi ngati chiboli yemwe adakhala pa kauntala akumwa mowa ngati ali kunyumba. Mwamuona akumwa mowa mtima uli pansi zoti pano nthawi ndi fili koloko mbandakucha sakulabadira. Ine bola ndinasiya kusangalala n’kubwera kunyumba thu koloko nde muzindinenanso? N’chifukwatu azibambo ambiri amangochezera kumowa ali yaponda yamwa.

Mkazi wa Katakwe sadadziwe choti ayankhe.

Inu mumakhala maso osagona ma BP atashuta chonsecho azimuna anu akungalula ma happy zotinso mulipo ataiwala kaye, Katakwe adatsendera. Phindu lake limakhala chani?

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

7 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *