Katakwe Kokaonekera

Katakwe

Kokaonekera

Wolemba: Lawrence Kadzitche

Tsikulo Katakwe ndi malume ake adatchena ndithu. Lidali tsiku lomwe Maria adalengeza kuti abwera ndi bwenzi lake kudzaonekerera. Thalauza lake latchekitcheki adali atalisita mpaka lidathwa ngati mpeni. Nsapato yake nayonso idali phuliphuli ngati ya wapolisi. Sikipa yake nayo idawala ngati matalala. Nawo a Topitopi adali m’suti ya mtundu wamtsiro yomwe inkatuluka panyengo zofunika monga potulutsa gule.

 

Kunja kudamveka kulira kwa galimoto, kutseguka ndi kutsekeka kwa zitseko ndipo kenaka kuodira. Alendo omwe ankadikira aja adatulukira. Maso a Katakwe ndi malume akewo atangogwa pa mlendo adafika ndi Mariayo, onse adawonetsa kudabwa komwe adakubisa mwachangu.

 

Mnyamata adafika ndi Mariayo adali wojintcha ngati anyamata onyamula katundu m’tauni. Mutu wake udali wampala koma wokhala ndi ndevu zoyala kuchibwano. Mmaso mudali magalasi omwe adasamira pamphuno ngati muja amachitira aphunzitsi a ku koleji. Adavala malaya osapisira ndi buluku la jinzi lokhwefula komanso lososokasosoka m’maondo. Mmkhosi adakolekamo matcheni pomwe mmanja mudali zibangiri.

 

“Takulandirani, apongozi,” a Topitopi adatero podziwa kuti mlendo sumuchita chipongwe.

 

Apo macheza adayamba. Monga momwe zimakhalira kokaonekera, mafunso ofuna kumudziwa mpongozi wawoyo adayamba.

 

“Tsono achimwene, mumatani?”

 

“Ndimathamangathamanga ma bizinesi m’taunimu,” adayankha mnyamatayo. “Mwa zina, ndimatolera ma renti mmanyumba a makolo anga, nthawi zina basi kuyendetsako makolowo makamaka mu magalimto a manual poti amawavuta,” adatero mnyamatayo.

 

“Zina mumatani?”

 

“Monga ndanena ndizambiri. Nthawi zina ndimathanso kutaiyitsa malo a makolo. Ndimapanganso u DJ ku night club ya ankolo anga.”

 

Katakwe ndi a Topitopi adayang’anitsitsana.

 

“Ankolo akewotu ali ku UK,” adalowererapo Maria.

 

“Yes, that’s true. Nde nthawi zina amanditumizira ngini yoti ndimatayitsa,” adatsimikiza mnyamatayo.

 

“Komanso siokhawo,” adaonjezera Maria. “Ena ali ku USA, ena ku South. Kwawo onse ndiochita bwino kwambiri. First born wakwawo ndi mphunzitsi ku univesite.”

 

A Topitopi adamunong’oneza Katakwe. Awiriwo adatuluka. Kenaka Katakwe adamukodola Maria. Atatuwo adakakumana kuseli.

 

“Chemwali, mukuti munthuyu mwamutola kuti?”

 

“Adandipatsa lift tsiku lina lake. Kwawotu ndikochita bwino kwambiri.”

 

A Topitopiti adagwedeza mutu. “Chemwali, mwamuna amayenera kukhala ndi chochita; pakhomo simuzikadya chikondi. Chikondi sichizikalipira lendi, ma fizi a ana olo mabilu akuchipatala.”

 

Msungwana sanaimve. “Nthawi zinatu amagulitsa malo a makolo ake…”

 

“Chemwali chimenecho sichochita: wamuna woti alibe chochita sayenera kukwatira,” Katakwe atero. “Uyu tamukana. Ngati mwamukonda mudzabwera nayenso akadzapeza chochita ngati bizinesi kaya ntchito.”

 

“Anthunu mwangokhala okonda chuma,” adalimbikira Maria. “Kale anthu ankakwatirana opanda…”

 

“Kale lake liti?” adafunsa a Topitopi “Ngakhale kale kuti munthu ukwatire umayenera kukhala ndi chochita china chake monga kulima, maganyu, kusaka…chinachake chobweretsa zofunika kusamalira mkazi ndi ana.”

 

“Malume…”

 

“Uyu tamukana. Mwamuna wofunsira mbeta kuti makolo amuvomere amayenera azikhala ndi chochita chogwirika osati, ‘Eee kwao nkotere, bambo ake, malume ake, achimwene ake, zamkutu!’. Tamapita naye galu wakoyo,” adatsendera a Topitopi.

 

End

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

4 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *