NYUMBA YA LENDI

Katakwe

NYUMBA YA LENDI

Wolemba: Lawrence Kadzitche

Tidali tinyumba tingapo tamakomo khumi. Kutiona munthu adakaganiza kuti tigwa nthawi ina iliyonse. Tidali tinyumba towonetsa kuti sitimasamalidwa. Bafa ndi chimbudzi chidali chimodzi chokha. Bafalo lidali loti lidagwa kumtundaku nde kuti munthu asambe amayenera kunjuta kapena kusamba usiku. Nacho chimbudzi chidali ming’alu yokhayokha choti munthu akamadzithandiza amaonekera ndipo pakhomo padali potsekedwa ndi chiguduli.

 

Katakwe ndiye adali mwini watinyumbato, landilodi pachingerezi. Anthu okhala panyumbazo adakhala akumupempha kuti akonze nyumbazo komanso awonjezere zimbudzi ndi mabafa pa pulotipo. Palibe chomwe Katakwe amachita.

 

Chomwe chidatsitsa dzaye ndichakuti Katakwe adalengeza kuti akufuna kumanga timanyumba tina towonjezera pamalopo. Matenanti aja adamuyitanitsa Katakwe.

 

“A landilodi, mukuti mukufuna kumanga tinyumba tina, nanga nkhani ya zimbudzi ndi mabafa ija ili pati?”

 

Katakwe adaseka. “A Dimioni, inuyo ndi wamkulu pa matenanti onse omwe ali pano; mukuona kuti mukufunsa funso la nzeru?”

 

Dimioni adaoneka kuti mutu udazweta ndi funsoli. Mmalo moyankha adamuyang’ana Katakwe modabwa.

 

Katakwe adatembenukira kwa matenanti ena omwe adali pamenepo. “Makosana, ndikudziwa kuti a Dimioni akulankhula mmalo mwanu. Koma mukuona kuti munaganiza mwanzeru?”

 

“Eya,” adavomera matenantiwo. “Paja takhala tikupempha kuti muonjezere zimbudzi ndi mabafa.”

 

Katakwe adaseka. “Aliyense mwa inu adabwera payekhapayekha. Pobwera munkati mukufuna chani?”

 

“Nyumba ya lendi,” onse adayankha.

 

“Tsono nkhani ili pati? Munkafuna nyumba ya lendi osati chimbudzi choti muzibibamo,” Katakwe adaunikra. “Munayenera kundiyamika kuti ndidakupatsani bonasi ya chimbudzi otherwise ndidayenera kukupatsani nyumba yokha.”

 

Ma tenanti adati dzidzidzi.

 

“Ngati landilodi udindo wanga ndiwokupatsani malo ogona osati obiba,” Katakwe adalongosola. “Malo ogona ndidapereka. Zoti muzisamba kapena kupambuka kuti sizikundikhudza. Mongokuthandizani mukhoza kumakapempha kwa maneba olo kumakadzithandiza kuntchito.”

 

“Zimenezo sizoona. Nyumba siyingakhale yopanda chimbudzi,” a Dimioni adatero.

 

“A Dimioni, nchaka ndimati nzeru zanu ndizochepa. Panyumba pano madzi mumakatunga kumjigo, bwanji simukuti ndizikupatsani ndine?” adafunsa Katakwe. “Ntchito ya landilodi ndikupereka malo ogona osati oyangala.”

 

End

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

6 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *