Katakwe
ABUSA CHEPETSANI KUDABADIKA
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Pali nkhani zina zomwe munthu amakana ngakhale atagwidwa kali kutsaya. Monga umfiti, munthu ngakhale atagwidwa akutamba palibe yemwe amavomera kuti ndi mthakati.
Motero mitu ya atsogoleri ampingowo idazweta. Ngakhale adali ndi umboni wokwanira pankhani yomwe amafunsayo, iwo adayembekeza kuti Katakwe akana.
“Abusa, takhala tikumva kuti mumapezeka m’malo momwera mowa nthawi yausiku,” funsolo lidatero. “Ndiye timafuna timve kwainu chilungamo pankhaniyi.”
“Ndizowona,” Katakwe adayankha mwachidule.
Akulu ampingowo adanong’onezana. A Mdzibwa, omwe ankalankhulira atsogolerowo, adati, “Ndiye titi chiyani poti malamulo a mpingo uno salola kutero?”
Katakwe adamwetulira. “A Mdzibwa, pali lamulo loletsa akhrisitu athu kepezeka pamalo omwera mowa?”
A Mdzibwa adakanda dazi lawo. “Mwina ndifunse mosapyatira kaya nditi mong’alula pobwereka kulankhula kwa masiku ano. Nkhani ndiyoti akuti inuyo mumapita kumabala kukamwa mowa,” a Mdzibwa adatero. “Ndipo anthu akhala akukuonani mukumwa mowa komanso mukuvina mutaledzera.”
“Apo tsopano mwafunsa bwino,” Katakwe adavomereza akugwedeza mutu ngati gulo. “Ndizoona ndimapita kumabala komwenso ndimakalawako chakumwa chaukali.”
Apanso akulu ampingowo adadzidzimuka ngati muja anthu amachitira mphenzi ikang’anipa mwadzidzidzi.
“Pepani abusa, sitikumvetsa; si inu nomwe omwe mumalalika kuti mowa ndi woipa?” adalowererapo a Milanzi. “Nde pamenepa mukufuna akhrisitu amve ziti?”
“Atsogoleri, ndikumvetsa nkhawa zanu. Koma mundiyankhe funso ili; kodi ku Russia ndikwabwino kapena koipa?”
“Sitikudziwa chifukwa sitidapiteko,” adayankha a Mdzibwa.
“Exactly my point. Ineyo kuti ndilalike zoona ngati mowa ndiwabwino kapena woipa ndiyenera kuulawa kaye. Kuti ndidziwe ngati m’mabala ndi mwabwino kapena moipa ndiyenera kulowamo kaye. Ndidziwa bwanji ngati kuledzera n’koyipa osaledzera kaye?” adafunsa Katakwe.
“Zimenezo mukhoza kuchita kamodzi…”
“Zochitika zimakhala zikusintha ndi nthawi. Sungati zomwe udaona mwezi watha zidakachitikabe. Motero apo ndi apo ndimayenera kukaona zomwe zikuchitika m’mabala kuti ndikamati malo amene aja ndioyipa ndizifotokoza ndili ndi umboni wogwirika,” adafotokoza Katakwe.
“Nanga kumwa mowako?”
“Nawonso mowa umakhala wamitundu mitundu. Ndiyenera kuyesa kuti uwu umaledzeretsa bwanji. Komanso kuona kuti ukaledzera chimachitika ndi chani. Zimenezi sizinthu zoti ukhoza kuchita tsiku limodzi. Komanso mowa wanyuwani ukunka nubwera, ndiyenera kumauyesanso.”
“Abusa..”
“Pakati pa akulu ampingo muli panonu, pali yemwe adalowako m’bala?”
Onse adakana molimba mtima. Katakwe adati, “Ine ndimachita ngati Tomasi Didimo, ndimapisa mmabala kukana kunena za mmaluwa monga kandimverere. Motero ine ngati m’busa wanu ndimapita mmalo omwera mowa kuti ndikaima pagome paja ndizikuuzani zenizeni za zochitika mmalo amenewa. Ndimalakwitsa pati?”
Palibe adayankha.
End
Nice composition
Thanks