Katakwe Receipt

Katakwe

Receipt 

Wolemba: Lawrence Kadzitche 

 

Zimachitika ndithu mmabanja ambiri. Mwamuna amatha kukhala ndi chibwenzi mkazi wake osanunkhiza olo pang’ono. Katakwe adali uja woti pachingerezi amatchedwa model husband. Pakhomo adali bambo wachikondi wodziwa kusamala banja lake. Kumpingo adali ndi udindo ngati mmodzi mwa alangizi.

 

Koma kuseri adali nkhandwe. Iye adali ndi zibwenzi zamseri. Pofuna kuti asagwidwe, iye ankachita zibwenzi ndi asungwana oyendayenda. Ubwino wa asungwana woyendayenda umakhala wakuti amasunga chinsinsi bola ukamawapatsa ndalama. Koma ukapanga chibwenzi ndi ena a ulemu wawo, nawo amafuna azidziwika ndipo ngakhale utakhala wochenjera bwanji pakhalekhale umadzagwidwa.

 

Katakwe ankakhala ku Nyambadwe ndipo bwenzi lakelo limakhala kwa Ntopwa. Motero padali povuta kuti mkazi wa Katakwe akhoza kukumana ndi msungwanayo ngakhale mwangozi. Akaweruka kunchito, Katakwe amakaimitsa galimoto yake panja pachisakasa cha msungwanayo nkulowa mnyumbamo kukacheza nkhani zakuya ndi buthulo.

 

Podziwa kuti adali pabanja komanso bwenzi lakeyo amatha kuchezanso ndi anthu ena, iye ankagwiritsa zishango nthawi zonse. Nthawi zambiri, msungwanayo amakhaliratu nazo zishangozo.

 

Tsiku limenelo adamuimbira foni bwenzi lakelo. “Madzulo ndikubwera kudzadya buya. Ngini ilipo?”

 

“Palibe. Ugule ukamabwera.”

 

Katakwe adakumbuka kuti padali katundu woti agulenso wakunyumba. Motero adadzera mu Shoprite kukagula katunduyo.

 

Makondomu amavuta kugula chifukwa munthu sufuna anthu akuone. Katakwe adawabisa pansi pa zina zomwe adagula ndipo naye wodinda adadinda mwachinsinsi nkumupatsira Katakwe receipt. Katakwe adaponya lisitilo mjumbo momwe munali katundu uja.

 

Adadzera kwa bwenzi lake lija ndipo uko awiriwo adacheza monga mwa masiku onse. Katakwe adakafika kunyumba ndipo mkazi wake sadalotepo kanthu.

 

Azimayi amaonetsetsa kena kalikonse. Akutulutsa katundu mujumbo muja adaona lisiti lija. Adayamba kuwerenga kuti aone mitengo yazinthu.

 

“Zinthutu zadula masiku ano…” Katakwe adatero osadziwa kuti kunja kulinji.

 

Adangodabwa nkhope yamkazi wake ikudetsana. Mwana wamkazi adakhuthula katundu yense pansi. Adaonetsa kuti akufufuza china chake. “Bambo, apa pakuonetsa kuti munagula makondomu. Ali kuti?”

 

Katakwe adati dzidzidzi. Adadziwiratu kuti nkhani imeneyi siyitha bwino.

 

End.

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *