Katakwe ZIYANG’ANA KUNGOLO

Katakwe

ZIYANG’ANA KUNGOLO

Wolemba: Lawrence Kadzitche

Pa Chichewa, zinthu zikathina, pali mawu ambiri omwe amanenedwa. Ena amati zafika pa mwana wakana phala. Chichewa china amati zafika pa mai wafinyira bere pansi mwana akulira ndi njala.

 

Pakulankhula pa anthu a chigawo chapakati, amati zayang’ana kungolo. Ng’ombe zikayang’ana kungolo, ngolo siyingayende.

 

Motero, nkhani idali itajokova, ng’ombe zitayang’ana ku dazibomu. Munthu ndi malume ake adatsala pang’ono kupindirana mashati.

 

“Ine ndikuti banja limeneli latha!” Katakwe adatero.

 

“Ine ndikuti banja limeneli silitha,” adatsutsa a Topitopi.

 

Katakwe adapuma mozama. “Malume, sindikukumvetsani. Maria ndi mwamuna wake akhala zaka akungokangana. Osatinso kukangana kokha koma akumenyana; ndiye mukuti choti banja lisathere ndichani?”

 

“Banja lidalengedwa ndi Mulungu m’munda wa Edeni motero munthu sangalithetse,” a Topitopi adatero. “Mulungu sangalenge chinthu choipa.”

 

“Malume, musayiwale Mulungu adalenga mphenzi koma imaphanso anthu,” Katakwe adaunikira.

 

“Amati wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino,” adalimbikira a Topitopi. “Komanso chomwe Mulungu walumikiza pasapezeke wina wolekanitsa.”

 

“Ine sindikulekanitsa,” Katakwe adatero. “Anthu adalekana wokha; anthu ongokhalira kumenyana nkumati ali limodzi?”

 

“Sungazimvetse, mphwangwa,” a Topitopi sadafune kugonja. “Mkazi ndi mwamuna akakwatirana amakhala thupi limodzi ndiye Mulungu sangalole kuti chiwalo chathupi chisiyane ndi chinzake.”

 

Katakwe adaseka. “Baibulo lomwelo limati ngati chiwalo chako chikukuchimwitsa chidule. Apa ziwalo zolumikizazo nzofunika kudula kuopa anthu kuchimwa.”

 

“Mawu a Mulungu ali apo, komanso pali ana,” a Topitopi adaonjezera. “Ana amavutika banja likatha…”

 

“Malume…”

 

“Komanso anthu aziti chani banja likatha…”

 

“Tsibweni…”

“Nkhani iyi yatha,” a Topitopi adagamula akutulutsa botolo lawo la kachasu ndikutayira pansi bibidayo. “Ine mwini mbumba ndikuti banja ili silitha.”

 

Motero banjalo lidapitilira Maria ndi mwamuna wake akungokhalira kumenyana ngati galu ndi mphaka. Sipadathe miyezi khumi pomwe uthengawo udafika. Pa ndewu yomwe idachitika pakati pa Maria ndi mwamuna wake, Maria adavulazidwa kwambiri ndipo adamwalira kuchipatala mmawa wa tsikulo. Mwamunayo adali m’chikwidzingo kupolisi.

 

“Paja malume mumati banjali lipitirire chifukwa pali ana,” Katakwe adawakumbutsa malume akewo. “Mmene mai awo amwaliramu ndipo bambo awo amangidwamu, awasamalira anawo ndi ndani?”

 

A Topitopi adangoti kukamwa pululu ngati chambo chouma.

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

  • Nkhani yabwino yosangalatsa ya phunziro.
    Koma yomvetsa Chisoni, mwina banjalikadathadi Maria sakadamwalira pobvulazidwa. Komanso amuna ake sakadamangidwa. Nthawi yomweyo Amalume awo amanena zoona kuti banja analidalitsa ndi Mulungu.
    Phunziro: kumvetsetsana kwabwino osati ndewu ayi. Ndewu siimanga mudzi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *