Katakwe LERO NDIKUKAPHA SING’ANGA

Katakwe

LERO NDIKUKAPHA SING’ANGA

Wolemba: Lawrence Kadzitche

“Ziti? Dolo ngati ine sindingalolere kuyaluka m’tauni muno chifukwa cha iwe,” adakalipa Katakwe. “Na ngati suvomera kuti tipite kwa sing’anga udziwe kuti banja latha.”

 

Mkazi wa Katakwe adagwedeza mutu. “Bambo mukudziwa bwanji kuti wosabereka ndine?”

 

Katakwe adaseka ngati zabwino. “Ukafunse kumudzi kwathu. Mimba sindinkati ndapereka liti. Kugwamula sindinkati ndagwidwa liti. Vuto lili ndi iweyo.”

 

“Bambo, asing’anga sindiwakhulupirira…”

 

Katakwe adamudula. “Ng’anga ndunenayo mpatali pankhani zosula. Dzina lake ndi Pompopompo chifukwa zake sizichedwa. M’tauni muno ngati anthu akubereka n’chifukwa cha iyeyo.”

 

Mwana wamkazi adapuma mozama. “Bambo, ine ndimaona kuti tingosiya zonse mmanja mwa Mulungu…”

 

Katakwe adamudulanso. “Mmanja mwa Mulungu! Vuto la pulani ya Mulungu sudziwa kuti idzatheka liti; munthu ukhoza kupempha chinthu lero adzakupatsa patatha zaka handede…”

 

“Bambo…”

 

“Osandidula! Ine ndilibe nthawi yodikira kuti tiziti Mulungu sachedwa kapena kufulumira. Ine anthu akundiseka kuti ndine mwachaje, gocho, ndidagwa mumpapaya panopa ndiye ndilibe nthawi yodikirira nthawi ya Mulungu yoti sidziwika kuti ndiliti,” adakalipa Katakwe. “Za sing’anga zimakhala za shuwa, za pompopompo. Ndiye zili ndi iwe, tipite kwa ng’anga olo banja latha.”

 

Ndani amafuna umbeta? Mwana wamkazi adavomera pofuna kupulumutsa banja. Motero, mmawa wa tsiku lotsatira adakapezeka pakhomo la sing’anga Pompopompo ku Masambabise.

 

Sing’angayo adali wakuda ngati mtsiro ndi wamutu waukulu ngati wakadzidzi. “Achimwene, inuyo mulibe vuto lina lililonse. Vuto lili ndi mayiwa,” adatero sing’angayo.

 

Katakwe adamuponyera mkazi wake diso la “ndinkati chiyani?”

 

“Ndiye kwa mayezi iwiri mayiwa azibwera kuno lachitatu lililonse kuti ndidzidzawapangira mankhwala,” adalamula sing’anga. “Ine ndine Pompopompo; ukatha mwezi uno mayiwa asadayime mudzanidule chala.”

 

Katakwe ndi mkazi wanga adavomera. “Chizimba,” adapitirira sing’anga Pompopompo. “Mayiwa azibwera kuno okha. Ndipo nthawi yomwe ali kuno inuyo bambo muzikadzitsekera kuchipinda nkumakupiza nsupa iyi.”

 

Iwo adapanga zonse monga adalamulira sing’angayo. Mkazi wa Katakwe akapita kwa sing’angayo, Katakwe ankadzitsekera kuchipinda n’kumakupiza nsupa ija mpaka mkazi wakeyo atabwerera. Monga mwa thamo la ng’anga ija, mwezi usadathe mkazi wa Katakwe adapezeka ali woyembekezera.

 

“Ndinkati chani? “adanyadira Katakwe. “Tsopano ndiziyenda m’mathalaveni mwa mgugu ngati shasha.”

 

Miyezi isanu ndi inayi idatha. Mwana adabadwa.

 

“Aise, tiye ukaone nthanga yanga kuchipatala,” Katakwe adamufutokozera mzake Likisho atalandira uthenga woti kwabadwa mwana wamamuna. “Ndinkakuwuza kuti ndine wobereka.”

 

Maso a Katakwe atagwa pa mwanayo nthumanzi idamugwira. Zidatheka bwanji? Nkhope ya mwanayo idali ndendende ndi ya sing’anga uja. Chimutu ngati cha chadzunda, kuda ngati chikuni chowauka…

 

“Aise lero ndikukapha sing’anga,” Katakwe adatero akutuluka m’chipatalamo mwa ukali. “Sangayende pansi dolo ngati ine motere!”

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

1 Comment

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *