Katakwe AMUYERETSA MMASO

Katakwe
AMUYERETSA MMASO
Wolemba: Lawrence Kadzitche

“Make mwana, tsegula,” adatero Katakwe ali dzandidzandi ngati nguli yoti nthawi ina iliyonse isiya kuzweta. “Wafika vwivwivwi mwana wahule!”

Mkazi wa Katakwe adatsegula. Katakwe adalowa akuwomba zikupa, mmaso mutada ndi bibida. Pakamwa padali nyimbo ya phuzo.

“Nsima ili kuti, galu iwe? Njala yatipha ife amuna wonyenga paliponse ngati galu.”

“Ili patebulo, bambo,” mkazi wa Katakwe adayankha mwa ulemu.

Katakwe adavundukula m’mbale. Iye adayang’ana zakudyazo ngati akuwona bibi. Adamuitanitsa mkazi wake.

“Kodi umandiyesa ng’ombe kapena mbuzi ine?

Mkaziyo anadabwa. “Bwanji, bambo?”

“Nanga nsipu uli m’mbalemu ngwandani?”

Mwana wamkazi adapuma mozama kuti atsitse mtima. “Bambo, pochoka pano simudasiye ufa kapena ndalama yandiwo. Ndachita kupanga ganyu kuti ndipeze chakudyachi; simungayamike pamenepo?”

Katakwe adamugenda mkazi wakeyo ndi ndiwozo. “Mkazi wopanda phindu iwe! Ndikamafika pano ndikufuna ndizipeza nyama apo bi ndizikadya kuzibwenzi!”

Mkazi wa Katakwe adalitaya tsonzi. Pakhomopotu ankangokhalira kufuna banja. Ntchito ya Katakwe kudali kumwa mowa ndipo sankathandizapo kena kali konse pakhomopo. Koma nthawi zonse akafika ataledzera ankafuna ndiwo zankhuli.

“Tsono akuti ndizizitenga kuti ndalama?” ankadzifunsa mwana wamkazi.

Chifukwa chodzifunsa funsoli pafupipafupi mayankho adayamba kubwera. Mayankho olakwika. Iye adakumbukira kuti padali amuna ambiri omwe adali wokonzeka kumupatsa ndalama bola kukonza kapansi.

Masiku otsatira Katakwe anadabwa kuti nthawi zonse ankapeza zakudya zapamwamba pakhomopo. Mpunga, tchipisi, nyama, chambo…

“Aise, anzako ndidakwatiwa n’kumbuyo komwe,” Katakwe ankabwekera kwa mzake Likisho. “Panopa mkazi wanga akundidyetsa bwino.”

“Bwanji? Wayamba geni?”

“Asi; akungothamanga maganyu,” adatero Katakwe. “Ndidamuopseza kuti ngati sindizipeza ndiwo za nkhuli ndizikadya kuchibwezi.”

Likisho adamuyang’ana mzakeyo modabwa. “Iwe ukuona kuti ndi zanzeru zimenezo?”

Katakwe adatulutsa mpukutu wa ndalama. “Dola tikumamwera masiku ano akumandipatsa ndi iyeyo. Ndilibe maswera; ndine vwivwivwi mwana wa hule.”

Sipadapite nthawi. Mwezi wachisanu Katakwe adafika tsozi lili mbwe. “Bwanawe, ndaona malodza,” Katakwe adalira. “Eti mkazi wanga uja ali ndi zibwezi…”

Likisho adaseka. “Nde ukudabwa chani? Iwe umati ndalama umadya zija amazitenga kuti?”

Katakwe adangoti ndwi ngati nkhuku yovumbwa.

“Nde usadandaule,” adatsendera Likisho. “Pajatu ndiwe vwivwivwi mwana wahule!”

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *