Katakwe Agwa Mmbuna

Katakwe
Agwa Mmbuna
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Amati fisi akagwa m’buna salankhula. Amaterotu chifukwa fisi akamapita kokaba mbuzi, amadziwa kuti nthawi ina iliyonse akhoza kukumana ndi zokhoma monga kulasidwa kapena kuphedwa kumene. Motero amayenda mokonzeka. Akakumana n’zokhoma amangoti mmwemo.

Koma momwe Katakwe ankapita kunyumba kwa Diniwe sankaganiza kuti akhoza kukakumana ndi vuto lina lililonse. Ichitu n’chifukwa chake atazindikira kuti wadzitsekera mu kabati sadangoti mmwemo. Nkhawa yowopsa idamugwira. Monga Tom mu katuni ija ya Tom and Jerry, Katakwe adatha kuona chiliza chake chitalembedwa kuti, “Pano pagona Katakwe (yemwe adamwalira atakhapidwa kuchibwenzi).

Nkhanitu idayamba masana atsikulo Katakwe atalandira foniyo. “Daling’i, mphaka wachokapo wakasaka mbalame ku Lilongwe,” adatero Diniwe.

“Ndiye abwere khoswe?” naye Katakwe adayankha m’chining’a.

“N’zomwe ndimayimbira,” adatero Diniwe. “Khoswe adzathe mtedza mtima uli mmalo.”

Atangomaliza foniyo, Katakwe adaimbira mkazi wake. “Make mwana, sindifika. Ndikupita ku Lilongwe kuli ntchito ina yake yadzidzidzi.”

“Bambo, mukuti ntchito zimenezi zimakhala bwanji zongokhala zodzidzimutsa. Mwezi watha munapita ku Mangochi…”

“N’chifukwatu ndimati kampani ino ndimafuna n’tasiya ntchito,” Katakwe adamudula mkazi wakeyo. “Ok, ndiye ndibwerako mawa.”

Adangoti zwee, n’kupezeka wakocheza kwa Diniwe ku Chinyonga. Katakwe adamasuka. Poti adalibe zovala zosinthira, adavala kabudula ndi malaya a mwamuna mzakeyo.

Atangolowa kuchipinda kogona mpomwe adamva kulira kwa galimoto. Diniwe posuzumira pazenera adaona kuti adali mwamuna wake.

Mantha adamugwira mwana wamkazi. “Amuna anga abwerera kaya chifukwa chiyani. Ndiyetu ngaukali zedi. Kungokupeza muno ndiye kuti akupha.”

Mtima wa Katakwe udadumpha. Iye adali atamva nkhani zambiri za anthu omwe adavulazidwa kapena kuphedwa kumene chifukwa chopezeka m’nyumba mwa mwini.

Mwana wamwamuna adaganiza mwachangu. Atani? Kenaka pulani idamufikira.

“Wachikondi, iweyo unamizire kuti wadwala kwambiri ndiye pakufunika athamange nawe kuchipatala,” adamutsina khutu bwenzi lakelo.

“Nanga akati alowe kaye?”

“No problem. Ndibisala mu kabati yazovalayi. Inu mukapita ine ndibulika basi wautali.”

Katakwe adadzitsekera mu kabati ija. Diniwe adatuluka akubuwula monga nkhumba. “Honey, ndadwala. Mtimawu ukuthamanga. Tiye undiperekeze kuchipatala.”

Mwana wamwamuna sadavutike n’kutsika, adangoti lowa, galimoto n’kuyitembenuza basi liwiro la ku chipatala.

Mukabati muja Katakwe adamva galimoto ija ikupita. “Yagwira!” adadzilankhulira akukankha chitseko cha wadilobuyo.

Chitsekocho sichidasunthe mpang’ono pomwe. Adachikankhanso mwamphamvu. Chidali nji ngati achikhomerera. Monga munthu woti watsitsimuka atamukhomera kale m’bokosi, adazindikira kuti chitseko cha kabatiyo chidali chotsegulira kunja. Adali atadzikhomera!
 
Sadakatha kuyimba foni poti adali atayiyiwala m’chipindamo. Iye adangoganiza zothyola chitseko cha kabatiyo ndi phewa lake. Koma chitsekocho chidali cholimba. Sichidathyoke. Ndi mantha onkera kumisala adayamba kuponda chitsekocho. Chitsekocho sichidasunthe!

Atani? Mtima wa Katakwe udakankha mwazi ngati uphulika. Adayenera kupeza njira yotulukira mu kabatimo mwamuna wa Diniwe asanabwere kuchokera kuchipatala ngati samafuna kukhala zovuta.

END

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *