Katakwe KU DANSI YA BURNING SPEAR

Katakwe

KU DANSI YA BURNING SPEAR

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Katakwe zidamuthina. Sadadziwe choti achite. Kuyambira pomwe adali ku sekondale, iye ankakonda kumvera nyimbo za chamba cha reggae ndipo Burning Spear adali mmodzi mwa oyimba a reggae omwe ankawakonda kwambiri.

 

Mnthawi yomwe adali ku sekondale kudutsa ku yunivesite anzake ankangomutchula Rasta KT chifukwa chokonda reggae. Nthawi zonse nyimbo zomvera zidali za reggae: Bob Marley, Peter Tosh, King Sounds, Culture, Burning Spear ndi oyimba ena otero.

 

Komatu ngakhale ankatchedwa Rasta KT, sikuti adali Rasta. Komabe poti anthu ambiri okonda reggae anthu amangowatchula ma Ras, nayenso adavekedwa dzina la Rasta. Akakondwa, Katakwe ankakhala nawo m’timagulu tosuta fodya wamkulu yemwe ma Rasta amamulemekeza pomutchula ganja kapena weed ndipo amati fodya ameneyu sadachite kuyitanitsa koma adamupeza akumera yekha pamanda a Solomo choncho ayenera kumugwiritsa ntchito. Motero, apo ndi apo, naye Katakwe ankafukiza mbanje.

 

Zaka zidapita. Tsopano Katakwe adali munthu wamkulu. Kuntchito adali bwana. Pakhomo adali mwamuna wamunthu ndi bambo wa ana asanu. Kutchalitchi adali mkulu wampingo. Akamalalika ankakamba kuti kale ‘tidali otayika ife, tikufukiza ndi kumvera nyimbo za achamba koma pano tidalandira Yesu ndipo tidasiya.’

 

Ngati kuphera mphongo mawuwa, akakhala pagulu nyimbo zomwe ankamvera zinkakhala za uzimu. Akamachotsa ya Great Angels Choir amakhala akuika ya Princess Chitsulo. Zabwino ndithu.

 

Koma monga momwe amakhalira anthu ambiri omwe pagulu amati ndi otembenuka mtima, kuseri amatsalirabe ndi tina mwa tizikhalidwe tawo takale. Akakhala payekha, kaya ndi mnyumba kapena m’galimoto, Katakwe ankayika nyimbo za reggae zija. Ngati watenga munthu, ankachotsa.

 

Motero atamva kuti Burning Spear akubwera, mutu wa Katakwe udazweta. Adayenera kupita kukamuonera. Koma apita bwanji poti ankati adasiya kumvera nyimbo za kudziko? Mosadziwa, naye mkazi wake adangotsekerezeratu ponena kuti, ‘Bambo a Dimi, kukubweratu woyimba wofukiza mudasiya kumvera uja; lidakakhala kale mudakapita koma lero zanu nza Yesu.’ Ndiye apa Katakwe adakatinso chani?

 

Katakwe adadya mutu. Atani kuti apite ku show ya Burning Spear koma mkazi wake asadziwe? Pulani iadamufikira. Adatsanzika kuti akupita ku meeting ku Mangochi.

 

Koma mmalo mopita ku Mangochi adabuthira bwa ku Lilongwe. Mmene show imayamba iye adali atafika. Adasintha zovala. Adavala t-Shirt yokhala ndi chithunzi cha Burning Spear pamtima. M’khosi adakolekamo scarf ya mtundu wa mbendera ya ma Ras. Kumutu adavala chipewa choluka cha makaka a mbenderanso ya ma ras chija chokhala ndi ma dread oluka. Adapezananso ndi anzake omwe adali nawo ku koleji omwe adamuninkha ka ganja kuti akumbutse chikale komanso akwezekonso ti ma bar ta molalo.

 

Zonse zidatha bwino. Katakwe adabwerera ku Blantyre mkazi wake osadziwanso kuti adaapita ku show. Mwina sadakadziwa mpaka kalekale. Koma paja adati chigwinjiri maliralira chidaulula msolo wambala.

 

Katakwe adali panja kucheza ndi mkazi wake pomwe mwana wake yemwe ankaonera TV adatulukira nkudzagwira mayi ake dzanja. “Amami, tiyeni mukaone munthu wofanana ndi adadi pa TV.”

 

Mkazi wake adalondola akuseka. Koma pobwerera, nkhope yake idali yodetsana ngati tsiku loti kugwa mvula yamkuntho. Adangofikira kumutengera Katakwe mnyumba nkuloza pa TV. Pokweza maso, Katakwe adaona kuti pa TV po ankabwereza show ya Burning Spear ndipo wa camera ankajambula iyeyo akuvina ngati woyimba adali iyeyo, ndudu ya ganja ikufuka mmanja.

 

“Chikatere, bambo a Dimi?” adalitulutsa funso mwana wamkazi.

 

End

 

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

3 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *