Katakwe
KOLAPA
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Zikafika potero, Chichewa chake amati mlaliki wayaka moto. Pobwereka kunena kwa omwe adakhalapo mkulu wa asing’anga, bambo Eliya, Katakwe adafika pa geji ina-ija yosiya kudya nsima ya pankhuni, nkumadya ya pa cooker, kusiya kusamba madzi ophitsa pamoto, nkumasamba a mu giza.
Kuli konse komwe iye amapangitsa msonkhano wachitsitsimutso kunkasonkhana fumbi la anthu lija ena amati la mwana ali pati. Anthutu amakhamukira ku misonkhano yake chifukwa cha ulaliki wogwira mtima womwe iye ankapantha. Ndipo patsikuli, monga mwa nthawi zonse, anthu adasonkhana mwa mzanga ali pati.
“Lero ndikufuna tonse tichitire umboni zachikondi chozama cha Mulungu,” Katakwe adagawa uthenga. “Chikondi cha Ambuye n’chopanda malire n’chaka ngakhale machimo athu atakhala ofiyira ngati magazi koma adzawayeretsa ngati matalala. Aleluya!”
“Aleluya!’ lidayankha khwimbi la anthulo.
“Ineyo ndidali woyipitsitsa. Ndi tchimo liti lomwe sindidapangepo? Ndidali wakhupha, chidakwa, wonyenga akazi a eni koma Ambuye adandigwira dzanja ndipo zonse ndidaleka. Ndiye ngati Ambuye adakhululukira chigawenga ngati ine n’kundisandutsa m’busa, machimo anu n’chiyani kuti asakhulukiriridwe?” Iye adapitiriza kulalika. “Aleluya!”
“Aleluya!” adalulutidwa
“Ndiye yemwe akufuna kulandira Yesu, afike kutsogolo kuno,” adalengeza Katakwe. “Musawope, Mulungu adakhululukira wodzozedwa wake Davide tchimo la chigololo ndiye angalephere kukhululukira agalu achabechabe ngati inu, a kafucheche oti enanu mudangobadwa chifukwa makolo anu adangochita dama pena pake!”
Anthu adakhamukira kutsogoloko. Katakwe adawasanjika manja nawapepherera.
Idafika nthawi yoti anthu apereke umboni. Mwa omwe adadzapereka umboniwo padali Khwethe. Katakwe adamuzindikira mkuluyo kaamba koti ankakonda kudzagulitsa makala pakhomo pake.
“Abusa , ndasangalala pondifotokozera za chikondi cha Mulungu. Panopa ndikufuna kuwulula chipsinjo chomwe chakhala chikundivuta ngati chilonda chakumsana,” adayamba motero Khwethe.
“Auze m’bale amvetsetse!” wina adakuwa m’chikhamu cha anthucho.
“Abusawa akhala akundichitira zabwino pondigula makala,” adapitiriza kufotokoza Khwethe. “Koma mmalo mowabwezera zabwino ine ndimawayenda pansi!”
“Fotokoza m’bale, Yesu akumasula!” munthu yemwe uja adafuula m’chigulu muja.
“Ineyo pakhomo pa abusawa mmalo mongogulitsa makala ndinkayendera zambiri. Ndinkagona ndi akazi awo.”
Bata lidagwa mwadzidzidzi pamsonkhanopo ngati kumasano. Anthu adangoti kukamwa pululu kulephera n’kutulutsa “iii” yemwe.
“Moti mwana wakuda ngati mtsiro uja ndidagenda ndine- “
Katakwe adamva mtima wake ukunyamuka n’kuyamba kuthamanga ngati chigayo cha dizilo. Mwadzidzidzi adachitsakamula chibakera chomwe chidagwa pakamwa pa Khwethe ngati hamala. Posakhalitsa adayamba kumuthira mvumbi wadzibakera mkuluyo. Zidatengera kulowerera kwa anyamata angapo adzitho kuti amugwire Katakwe.
“Sangandipusitse motere,” adakalipa Katakwe akupuluputa ngati mlamba. “Ameneyu ndithana naye. Mkazi wanganso adziwiretu kuti banja latha.”
“Abusa, mmayesa mumati mfumu Davide…”
Funsolo Khwethe sadalimalize chifukwa adalandiranso chibakera china. “Ndiye ine ndi mfumu Davide?” Katakwe adafunsa akunjenjemera ndi ukali.
“Inetu ndimati ndikulapa,” adabuwula Khwethe magazi ali chuchuchu.
END
Tsonotu mwatitengetsa ngt amisala kumaseka mu msewu????????????????
I love that part wen katakwe wafusa kut tsono ine Nd mfumu decide????????????????
Ha ha ha ha ha zibagela zake ngati za IP-man kapena Muhammad Ali,
Kkkk zinthuzi zalowa personal mu uzimu zija zatuluka