Katakwe
ZINA ZIKATI ZICHITIKE
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Pali mavuto ena omwe munthu umagwamo osati chifukwa choti walakwitsa koma chifukwa chakuti zikuoneka ngati walakwitsa. Zimakhala zoti ngakhale utafotokoza bwanji, palibe yemwe angavomere kuti ukunena zoona.
Izi Katakwe adatsimikiza tsikulo atakwenyedwa ndi Bayisoni. Banja la Katakwe ndi Bayisoni lidali logwirizana kwambiri, mabanja aja pachingerezi amatchedwa ‘family friends.’ Mabanja awiriwa ankachezerana bwino kwambiri. Iwowa ankakhala mu lokeshoni imodzi pamtunda wokwanitsa kuyenda pansi.
Zikati zinthu zilakwike zimayambira patali. Tsikulo kudatentha kwambiri ndipo Katakwe adaganiza zokamuona mzake Bayisoni kuti mwina akhoza kukaolombya kukhosi pabala ina yake. Atapita kuti akamutsanzike mkazi wake, adamupeza ali mtulo tamasana. Posafuna kumusokoneza malinga nkutenthako, iye adangowauza ana kuti ‘mai anu akadzuka muwauza ndapita kwa Bayisoni.’
Kunja kudali ngati mung’anjo yamoto. Ngakhale sipadali patali, Katakwe adakafika thukuta likuyenderera. Monga momwe ankachitira pachinzawo, atafika kwa Bayisoni, iye adangofikira kulowa amvekere, ”Bwanawe, tuluka kuchipinda afika mashini oyendera mphepo,”
Koma adatuluka adali mkazi wa Bayisoni atavala chitenje chomangira mkhwapa. “Kodi ndi mula; ndimatitu tizikasamba malinga nkutenthaku,” mkazi wa Bayisoni adatero akukamula thukuta.
“Kwawotchadi, mula,” Katakwe adavomereza. “Iwe kasambe. Tandiyitanira mchimwene.”
“Amenewotu mwasemphana.”
“Wapita kuti?”
“Basi anangoti akubwera,” adayankha mkazi wa Bayisoni.
“Nde basi ndikupita,” Katakwe adatero. “Nkalume ungapo wamame malinga ndi dzuwali.”
Mmimba simupanganika; Katakwe adamva mmimba kutentha. Adapita mu chimbudzi cha myumbamo nkukadzithandiza.
“Zatheka, mula,” iye adatero akutsanzika.
Akutuluka adangoti gululu ndi Bayisoni. “Aise, ndimanyamukatu.”
“Ndafika, tiye bwerera,” adatero mzakeyo mwansangala. Kenaka Katakwe anadabwa mzakeyo nkhope itasintha.
“Galu iwe, ndi zomwe umachita ine nkachopa?” Bayisoni adafunsa mokwiya.
Katakwe adadzidzimuka. Adalakwitsa chiyani? “Ndimatani?”
“Ineyo ndimakutenga ngati mbale wanga, mchimwene wanga koma ungamandinyengere mkazi wanga?”
Katakwe sadamvetse kuti mlanduwu umachokera pati. “Bwanawe, wekha ukudziwa kuti sindingachite zoterozo.”
“Amwene, padziko pano palibe chinsinsi. Lafote limafika lokha,” adatero Bayisoni. “Lero mwatchera kutawala mwezi nkhanga zawona.”
“Zimenezo sizoona…”
“Kumeneko ndike kukanana kali kutsaya. Nanga bwanji zipi wako ndi wotsegula?”
Apa mpomwe Katakwe adaona kuti adayiwala kutseka zipi atamaliza kudzithandiza mu chimbudzi muja.
“Nanga bwanji mkazi wanga wavala chitenje chokha?” adapitirira kufunsa Bayisoni.
Katakwe asadayankhe Bayisoni adapereka chigamulo. “Anthu munali awiri; iwe ukutuluka zipi wosatseka, mkazi wanga wavala chitenje chokha, nonse muli thukuta chuchuchu – palinso chofunsira kuti mumatani?”
Apa mpomwe Katakwe adazindikira kuti ngakhale atafotokoza bwanji, mzakeyo sangamve.
END
Kkkkk inalidi nkhani yovuta mayankhidwe
Yongofunika kukhala chete