Katakwe
PALIBE CHINSINSI
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Pali amuna ena amangoti yagwa m’mbale n’ndiwo. Amuna amenewa sasankha pankhani ya azimayi. Amangoti bola wavala siketi.
Katakwe adali m’gulu limeneli. Iye adali ndi zibwenzi zambiri. Ena adali omwewa aja amaima mmisewu nthawi yausiku. Azimayiwo ankakumana nawo ku resitihausi ina yotchipa yomwe ntchito yake kwambiri siyidali yogonako koma yochitirako chisembwere.
Sikutitu Katakwe sadali pabanja. Adali pabanja ndithu. Komanso sikuti adangokwatira mkazi woti bola amavala andiloko. Mkazi wake adali mayi wakumaso kwa anthu. Woumbidwa ngati fulufute, adali mkazi uja amapangitsa amuna kuomba mtengo chifukwa chokanika kuchotsa maso. Koma poti amuna ena kaya chimakhala chiwanda kaya chani, Katakwe ankathawa getsili ndikumakakumana ndi amayi oti amaoneka ngati Mulungu adawalenga atatopa.
Poti ku resitihausi ankapita kuja kudali koti mkazi wake sangapiteko, Katakwe adaona kuti zake zidali bwino. Padalibe njira yoti adakagwidwira. Kuonjezera apo, chifukwa chopitapitako, mnyamata wa pa reception ankacheza naye bwino ndipo monga kasitomala wamkulu, ankadziwa kuti mnyamatayo sangamuulule.
“Mtchini wafika,” mnyamatayo ankatero Katakwe akafika. “Kuperesa mphale non-stop mosayang’ana nkhope.”
“Chigayo choyendera mphepo,” Katakwe ankatero. “Palibe zoti magetsi azima kapena dizilo wasowa.”
Nthawi idapita. Munthu amasintha. Katakwe adalandira Yesu ndipo adasiya zazibwenzi komanso zotenga mahule. Motero ku resitihausi kuja adasiya kupitako.
Komabe amati pakhalekhale zomwe munthu amachita zimakhala ndi zotsatira zake. Mmoyo uno kapena winawo. Katakwe adaziona mmoyo womwe uno.
Tsikulo adapita kokasangalala ndi mkazi wake ku Mangochi. Kumeneko adaganiza zokagona ku loji ina yomwe idali itangotsegulidwa kumene mmbali mwa nyanja.
Katakwe sadamuzindikire mnyamatayo koma mnyamatayo ndi yemwe adamuzindikira.
“Biggy!” mnyamatayo adatero. “Welcome!”
Katakwe adaluka nsidze. Mnyamatayo adali mu suti yapamwamba ya pa reception. Adakumanapo naye kuti? Zomwe adanena mnyamatayo ndi zomwe zidamukumbutsa.
“Man, mwapangatu upgrade zonse,” mnyamatayo adatero mwansangala. “Mwatenga katundu wabwino komanso kubwera naye kumalo abwino.”
Apa mpomwe Katakwe adakumbukira kuti adali mnyamata ankagwira ntchito ku loji uja. Mnyamatayo adapitiriza. “Ndinkadabwa kuti biggy ngati inuyo bwanji kumafika kumene kuja komanso mutatenga nyangwita. Uyu ndiye katundu genuine. Kukhala nyumba tidakati self-contained komanso yokhala ndi boys quarter; kupita uko mzimayi, kubwera kuno mzimayi.”
Katakwe adadziwa kuti mnyamatayo samadziwa kuti wabwera ndi mkazi wake. Pofuna kuti asapitirire kulankhula, iye adatuluka mwachangu kunamizira kuti akukayankha foni. Adakadziwa sadakatero.
“Mayi, inuyo ndiye mukukhalana ndi bwanawa. Osati zomwe ankabweretsa kale. Inu ndi katundu wa label,” mnyamatayo adadukiza namuzungulira mkazi wa Katakwe. “No mistake. Apa bwana adya katundu wowayenera.”
Mkazi wa Katakwe anadabwa. “Ankatani bambowa?”
“Bambo ameneyu ndi wachisika heavy. Ndikugwira ntchito ku loji ina ku Blantyre ankati wabwera wabweranso ndi azimayi. Komatu azimayi ake zinkakhala nyangwita ngati zotola pa kaunjika koma pa inu zili bho.”
Katakwe adatulukilanso akuganiza kuti mwachangu ayambitsa nkhani ina mkazi wake asadatolere kuti mnyamatayo amati chiyani. Koma atangofika mnyamata uja adati, “Biggy, ndimawafotokozera mayiwa kuti pano mwakweza geji si zimbayambaya munkabweretsa ku loji ya ku Blantyre. Uyu ndiye katundu wokuyenerani.”
Katakwe adayang’ana mkazi wake. Yekha mantha adamugwira ndi momwe nkhope ya mwana wamkazi idadetserana. Adakakhala olemba nthano adakati Katakwe adalakalaka kuti pansi pang’ambike abisalepo. Koma izi zidali zenizeni motero pansi sipadang’ambike. Ngati kutulo adaona chibakera cha mkazi wake chikubwera mothamanga kulondola mutu wake. Mmene Katakwe ankatsitsimuka, adali ali kuchipatala.
END
Mbiri imakutsatila Munthu ????????????????????
Atagwira kolona wake munthu wa Mulungu adakuwa ‘mukundiphelanji?’
Kkkkk…. This is a very nice story