Katakwe
GALIMOTO
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Magalimoto alipo a mitundu iwiri. Ena oti bola kukafika ndi ena oti amalankhula. Katakwe adafika pagalimoto yolankhula, galimoto yapamwamba. Idali yamtundu wofiyira ndipo idali phuliphuli mdzuwa la tsikulo ngati nsapato ya munthu wapolisi.
“Aise, waona makina omwe ndagula?” Katakwe adanyadira kwa mzake Likisho.
Sadadikire kuti mzakeyo ayankhe. “Mashini apamwamba. Kuliza kungotsina apa. Full automatic. Ma speaker ngati a pa show. Leather seats. Speed ngati ya ndege.”
“Aise, koma mutu wako umayenda?” Likisho adafunsa.
Katakwe anadabwa ndi funsoli. “Bwanji?”
“Apapa ukuona kuti wachita zanzeru?”
Mizere idaoneka pachipumi pa Katakwe. “Sindikumvetsa.”
“Iweyo ulibe nyumba ndiye ukuona nchanzeru kuti ugule galimoto?”
Katakwe adamuyang’ana mzakeyo modabwa. “Eya nchanzeru.”
Likisho adaseka. “Munthu uli pa lendi, ulibe olo chisakasa, nkumaona kuti wachita chanzeru kugula galimoto, osangotinso galimoto dzina koma yodula kwambiri?”
Katakwe adaseka. “Aise chilichonse chili ndi nthawi yake. Ndidakali mnyamata panopa ndiye ndi nthawi yoti ndinjoye. Moti iyiyi ndikafika pamalo yokha izifotokoza kuti pafika biggy. Ndagulanso foni yoti ndikangoyiponya pa kauntala mubala aliyense azidziwa kuti pafika munthu.”
“Bwanawe, kuganiza koperewera kumeneko. Anzako pano tagula puloti posachedwa tiyamba kumanga.”
Masiku adapita. Amati ukatchula mkango kwera mumtengo. Ulendo woyamba Katakwe adamudutsa mzakeyo kukugwa mvula yamkuntho, “Tadutsatu,” Katakwe adakuwa akudutsa. “Anzathu paja mumakwera puloti.”
Sipadapite nthawi; Katakwe adalandira foniyo pakati pa usiku. “Aise, mwana wadwala ndiye ndimafuna ubwere udzanditenge tipite kuchipatala.”
“Ukunena zimenezo ndiwe? Bwanji osangokwera puloti ija?” Katakwe adafunsa.
“Kukwera puloti?”
“Eya. Olo nyumba ukumanga ija…”
“Bwanawe, pepa…”
“Ndikubwera kudzakutenga,” Katakwe adamudula. “Koma choti udziwe nchoti anthu mumalankhula mopusa. Nthawi zonse mumangoganiza kuti nyumba yokha ndiyofunika. Nchifukwa ena amafunsa kuti kugula pizza ndi thumba la simenti chofunika ndi chani. Opusa amati thumba la simenti. Amaiwala kuti pizza yemwe sudya lero sudzadyanso mpomwe simenti ukhoza kugula nthawi ina iliyonse. Olo utati udzadya mtsogolo umadzapezeka ndi BP olo shuga basi gemu yagona.”
END
Ma wise okhaokha, case closed ???? .
Case closed.
Ndipo zoona moyomu mumangofunika kupanga chomwe ukuona kut ndi chamzeru apa moyo wako zomwe zingakusangalatse cz chilichose nchabwino zimatengela nthawi
well said