Katakwe Akwenyetsa bwana

Katakwe
Akwenyetsa bwana
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Sichachilendo. Madilayivala ambiri amakonda kunamizira kuti ndi mabwana. Akakhala kuti amayendetsa General Manager, nayenso amavala udindowu. Izitu zimakonda kuchitika makamaka akakumana ndi asungwana.

Katakwe adali dilayivala wa General Manager wa Chimanga Commodities ku Old Town. Koma akakhala kuti ali yekha samakhalanso dilayivala. Iye tsopano amanama kuti ndi General Manager.

Galimoto yomwe ankayendera idali yapamwamba zedi. Pali zinthu zitatu zomwe zimakopa asungwana ngati agulugufe ku magetsi a galimoto. Ziwiri mwa izo ndi galimoto ndi ndalama. Motero ngakhale Fiona adali pabanja adatengeka ndi bodza la Katakwe loti adali bwana komanso galimotoyo idali yake mpaka adamuvomera Katakwe ubwenzi wamseri.

Mwamuna wa mkaziyo ankagwira ntchito yomwe inkamuchotsa panyumba pafupipafupi. Motero Katakwe samavutika kupeza danga lokumana ndi wachikondi wakeyo.

Nthawi idapita. Ndiye monga sizilephera pankhani yachibwenzi chamseri, mwini mkaziyo adamva kuti pakhomo pake pamafika mkulu wina ndi galimoto ya mtundu wa Mercedes Benz kudzabwira nsinjiro zake. Adapatsidwanso nambala ya galimotoyo.

Mwana wamwamuna sanadikirenso kuti adzagwire yekha awiriwo ali mchikondi. Adangoyamba kusaka galimotoyo mtauni.

Loweruka lina bwana uja akutuluka mu sitolo ina ku Bwalo la Njovu limodzi ndi mkazi wake anadabwa kuona mnyamata wina atayima pagalimoto yake, chikwanje chili mmanja.

Mwini wake wa galimoto iyi ndiwe? adafunsa mnyamatayo.

Bwanayo adavomera.

Aha, ndiye lero watha, adatero mnyamata uja akusamula pwitika uja.

Bwanayo adakatemedwa pachipanda mkazi wake kulowerera. Achimwene, mukuti amuna angawa amatani?

Mayi, mdala wachisembwereyu akuyenda ndi mkazi wanga, adatero mnyamatayo. Ndiye lero ndimugaza koopsa.

Kudabwa kudaoneka pankhope ya bwanayo. Kuyenda ndi mkazi wako? Ine ndilibe chibwenzi china chilichonse chamseri.

Ndilibe chibwenzi chilichonse! adatero mnyamata uja monyodola. Sindiwe Katakwe, General Manager wa Chimanga Commodities?

Kuzindikira kudagwa pankhope ya bwanayo. Ndinedi General Manager wa kampaniyo koma dzina langa si Katakwe. Katakwe ndi dilayivala wanga. Kwerani galimotoyi tikalondoloze nkhaniyi.”

Katakwe ataona bwanayo akutulukira ndi mwamuna wa bwenzi lake lija adadziwa kuti mphaka wajowa m’thumba. Sadadziwe kuti zimuthera bwanji.

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

1 Comment

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *