Katakwe KULALIKIRA M’CHINGEREZI

Katakwe

KULALIKIRA M’CHINGEREZI

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Monga mkhalakale mu chikhrisitu, a Topitopi amadziwa kuti zimatheka munthu kusintha khalidwe. Iwo sadali mkhirisitu chabe komanso mkulu wampingo ndipo mu baibulo lawo mudali zitsanzo zambiri za anthu omwe adasintha kuchoka kumoyo wachionongeko kupita ku chipulumutso. Zakeyo and Paulo zidali zitsanzo zabwino.

 

Koma nkhani yomwe idawapeza siyidali yoti Katakwe wasintha chabe. Ayi. Iwo adauzidwa kuti mphwawoyo adatembenuka. “Sikuti adangolandira Yesu kokha komanso panopa akutsogolera mpingo womwe adayambitsa yekha,” Likisho adatero.

 

Akadamva mawu a mzukwa sadakadabwa. Katakwe kutembenuka? Kuyambitsa mpingo mpaka kukhala mbusa? Monga Tomasi Didimo, a Topitopi adaganiza zokapisa m’mabala.

 

Motero sabata yotsatira, Likisho adabwera kudzawatenga a Topitopi kuti akapemphere nawo ku mpingo wa Katakwe. Monga adagwirizirana, Katakwe sadamuuze.

 

Mpingowo udali mkati mwa lokeshoni. Kuchokera patali, a Topitopi sadathe kusiyanitsa tchalitchilo ndi chigafa chafodya. Koma chodabwitsa panja padali magalimoto angapo a pamwamba.

 

“Mercedes Benz yo ndi ya Katakwe. Magalimoto atatu enawo ndi a atsogoleri a mpingo,” Likisho adafotokoza.

 

Adapeza mapemphero ali mkati. Atangolowa, a Topitopi adaona kuti chinachake sichinali bwino m’nyumba ya Yehovayo. Choyamba, chidali mphwayo ankati ndi mbusayo. Mwina kuti mukhale ndi chithunzi chabwinobwino, Katakwe ankangooneka ngati mbusa uja adali mu filimu yotchedwa Coming to America. Kwa omwe simunayionereko, iyi ndi kanema yotchuka yopangidwa ku America ndipo masiku ano mukhoza kuionera mosavuta pa internet.

 

Chabwino. Katakwe adali mu suti yonyezimira yokhala ndi maluwa yomwe padali povuta kudziwa ngati idali yachimuna kapena yachikazi. Nako kuphazi kudali nsapato yosongoka yamtundu wachikasu. Kumutu adali ndi tsitsi lambiri lamzindo lomwe limaonekeratu kuti lidali lothira mankhwala. Mwachibadwa, Katakwe sadali woyera koma tsopano nkhope idali yoyera-osati yoyera koma titi yofiyira. Sipadali pofunika kufunsa kuti munthu azindikire kuti kuwezuka kokhala ngati tomato wosapsa bwinoko kudali kochokera mmafuta oyeretsa khungu.

 

Chidali chani munthu wa Mulungu kuvala ngati ali pa drama? Munthu wa Mulungu kumayuza, pobwereka Chichewa cha masiku ano? Tsitsi kujelula ngati mzimayi?

 

Adakadzifunsa izi, a Topitopi adadzidzimukanso kuti Katakwe sankalalikira m’chichewa. Mphwawoyo ankalalikira m’chingerezi wina nkumatanthauzira m’chichewa. A Topitopi sadamvetse. Onse omwe adali mkachisimo adali anthu akuda, cholalikira m’chizungu chidali chani?

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

5 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *