Katakwe KABAZA

Katakwe
KABAZA
Wolemba: Lawrence Kadzitche

“Bwanawe, masiku amenewa takhala tikusemphana ngati tidatemera msemphano,” Likisho adatero atafika pakhomo pa Katakwe.

“Aise, pajatu ndidayamba bizimezi ya kabaza,” Katakwe adayankha “Ndikakhala kuti sindili kumsewu ndikumakhala ku video show.”

“Ukumakataniko ku video show?”

“Kuonera ma filimu a madolo odziwa kuyendetsa mithuthuthu.”

Likisho adaseka. “Koma nawenso! Zimenezo zikhoza kukuthandiza chiyani?”

“Aise, ndikumaphunzira mayendetsedwe anjinga mwaudolo. Panopa ndikamayendetsa ukhoza kuganiza kuti ndine Dule kapena James Bond.”

Likisho adasekanso. “Aise ndinangoti ndidzakuthire diso. Apa ndulowa m’tauni.”

“Tiye ndikuperekeze ulaweko mashini anga,” Katakwe adatero.

Awiriwo adakwera. “Chipewa bwanji?” adafunsa Likisho.

“Aise, izi n’za maninja, sitivala helemeti,” Katakwe adayankha akuliza njinga ija.

Adanyamuka ngati ali pa mpikisano. Mu malokeshoni mumakhala anthu ambiri koma Katakwe ankathamanga ngati alipo yekha. Likisho adangoti khuma kumbuyo ndi mantha ngati nkhuku ya chitopa.

Atafika polowera mumsewu waukulu wolowa m’tauni, Katakwe sadayime kuti ayang’ane uku ndi uku. Adangolowa kulunjika m’tauni. Iye ankayendetsa njinga yamotoyo osasamala za magalimoto kapena a njinga ena. Overtake ankapangira mbali ina iliyonse, kumanzere olo kumanja. Nthawi zina ankalowa pakati pa magalimoto. Akamasintha mbali yoyenda, samavutika kuyang’ana kumbuyo kuti awone ngati kukubwera magalimoto. Pamalo pena adalowa pakati pa magalimoto ndipo ma handulo adakanda galimoto imodzi.

“Aise, imitsa njinga,” mwamantha, Likisho adatero.

“Bwanji, bro?”

“Ndati taima,” adabwereza Likisho mokwiya.

Katakwe adapatuka ndikuimitsa pambali. Likisho adatsika.

“Kodi anthu oyendetsa njinga zamoto kuyendetsa kumeneku kumakhala kwa mtundu wanji?”

“Bwanji?”

“Mumayendetsa ngati mulibe bongo olo muli ndi ‘death wish’. Kaya mumaonera kwambiri ma filimu, mumayiwala za mufilimu sizenizeni. Zotsatira zake mumapangitsa ngozi.”

“Aise, ngozi ndi ngozi…”

“Inde ngozi ndi ngozi koma ngozi za anthu a kabazanu zimakhala zopeweka. Wani, mumayenda pamsewu opanda ma helemeti. Thu, mumayenda pamsewu osatsatira malamulo komanso mutanyamula anthu ambiri; mumaganiza bwanji?” adafunsa Likisho. “Ngati mumafuna kudzipha muzingodzimangilira mmalo mopangitsa ngozi anthu ena.”

“Aise, imeneyi ndi geni,” adalongosola Katakwe. “Tikanyamula anthu anayi imawinira kudimba. Komanso tikamapanga ma overtake aja timakafika msanga ndekuti timapanga dola yambiri.”

Likisho adagwedeza mutu. “Mukachita ngozi?”

Katakwe adangoti kukamwa pululu ngati chambo chouma.

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *