Katakwe Chinyengo Chimugwetsa Mmavuto

 

Katakwe

Chinyengo Chimugwetsa M’mavuto

Wolemba: Lawrence Kadzitche

Katakwe adamuona koyamba mayiyo nthawi ya zopereka. Chidamuchititsa chidwi choyamba chidali mayendedwe ake. Sadasiyane n’kuti ali pa catwalk ya fashion show. Pokweza maso ake kuchokera kuphazi adawona kuti mpaka adafika pabondo osaona siketi. Siketi adayipeza ataona kale ntchafu. Kuchoka apo maso ake adagwa pankhope ya mayiyo; adali chiphadzuwa.

Munthu wamayi adaponya ndalama m’mbale. Katakwe adayesa kuthawitsa maso ake-adalephera. Mokhala ngati akuonera kanema maso ake adaperekeza mayiyo atamatirira pambuyo yake yomwe inkagwedezeka ngati ikuti abusa ndimakukondani, abusa ndimakukondani.

Sizidamutengere nthawi-tsiku lomwelo adadziwa pomwe mayiyo amakhala, kuti adali pamphala ndipo adakamuyendera madzulo ake. Mmene imatha sabatayo n’kuti Katakwe atafotokoza kale mawu akukhosi kwake.

Adia, mayiyo, adamuyang’anitsitsa Katakwe. “Nanga abusa, poti muli pabanja?”

“Zikutanthauza kuti Mulungu akundiuza kuti ndidakwatira mkazi wolakwika,” adatero mopanda manyazi Katakwe. “Nthiti yanga ndiwe.”

Adia adati khosi khoba. “Nanga n’ti cha? Ndine ndani kuti nditsutse chokonza Ambuye?”

Motero, polengeza kuti m’tchalitchimo mwafika mlendo, Katakwe adati, “Mtchalitchi muno, ambuye atitumizira nkhosa yakhama kwambiri. Mayi taimirirani,” Adia adayimirira. “Mayiwa komwe adaliko adali olimbikira kwambiri. Ndiye kuno paja otsogolera bungwe la amayi adasamuka, iwowa ndiye alowe m’malo mwawo.”

Ubwino wokhala mbusa, anthu sakutsutsa ngakhale upange zoti sakugwirizana nazo. Amakangolankhulira kuseri. Motero Adia adakhala chair lady wabungwe la amayi.

Padali posavuta kuti awiriwa akumane. Katakwe akapita kunyumba ya Adia amangokhala ngati akuyendera za mpingo. Akakhala limodzi m’galimoto zimangokhala ngati za mpingo.

Koma padali vuto limodzi. Adia adali wokonda ndalama. Nthawi zonse ankangokhalira kupempha ndalama ati zopititsira patsogolo bizinesi yake. Kudapezeka kuti Katakwe adayamba kuba ndalama za mpingo kuti azipatsa Adia. Oyang’anira chuma cha mpingo adayamba kudabwa. Pokasuzumira mthumba la tchalitchi adapeza mulibe kanthu. Katakwe adali atatapa ndalama zonse. Adayitanitsidwa.

“Abusa, tapeza kuti kuthumba kulibe kanthu; mungatifotokozere kuti ndalama zidayenda bwanji?”

Katakwe adauzidwa kuti abweze ndalamazo apo bi amuvula ubusa ngakhale kumumangitsa kumene. Iye adangoti ndalamazo zilipo ndipo abweza tsiku lotsatira. Adapita kunyumba kwa Adia kuti akapemphe kuti amubwereke ndalama zoti abwezezo. Adapeza panyumbapo pali pululu.

“Kodi mayi amakhala m’nyumba iyi aja apita kuti?” adafunsa mkulu wanyumba yoyandikana nayo.

“Asamuka lero mmawa. Sadanene uko apita.”

Mtima wa Katakwe udayamba kuthamanga. “Amachita bizinesi. Kaya mungawadziwe malo omwe amachitira bizinesiwo?”

Mkuluyo adamwetulira. “Bizinesitu ankachitira pompano, ngatitu n’kuyitcha bizinesi. Pamati pakamachoka mwamuna uyu, pakubwera wina,” mkuluyo adadukiza namuyang’ana Katakwe mwachidwi. “Tadikirani pang’ono, inu sim’busa uja amabwera pano uja?”

Katakwe adavomera.

“Pochoka anati nduthawa kam’busa kena kake, ndakadula. Sindikukaika kafika akakathinitsa kumpingo.

Apa mpomwe Katakwe adatseguka m’maso. Adangoyamba kulira.

end

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *