Katakwe Achimwene, Mwayamba Zisudzo?

Katakwe

Achimwene, Mwayamba Zisudzo?

Wolemba: Lawrence Kadzitche

Tsikulo, pochoka kunyumba, Katakwe adatsanzika kuti akukachita umodzi pabalayo. Mkazi wake, monga mayi womva mwambo, adamulola. Koma m’malo mongoyendera nzengo monga adatsanzikira, sakhwi adali atatsamira paphewa lake m’balamo. Uyutu adali Psa Mbalame, hule lomwe lidali bwenzi lake pabalapo.

 

Zina kambu, akuluakulu amatero zikadabwitsa. Ati powonetsa chikondi, iwo ankamwera mu botolo limodzi la mowa. Wina akamwa, ankapatsa mzake kuti apsonthekonso. Nthawi zina wina amamwa n’kulavulira mkamwa mwa mzake ngati mbalame ikamadyetsa ana.

 

Kuwonjezera apo, Katakwe adasinthana zovala ndi hulelo. Pomwe iye adali m’bulauzi la buthulo, msungwanayo adavala shati yake. Nako kuphazi kwa Katakwe kudali gogoda pomwe namwaliyo adavala masandasi a Katakwe. Kumutu Katakwe adavala kachipewa ka mtsikanayo pomwe namwaliyo adavala kapusi yake.

 

Zidali zoseketsa kuziwonera patali koma iwo adalibe nazo kanthu. Anthu akakhala m’chikondi-chamumdima kaya chapoyera-m’maso mumada ndipo m’makutu mumagontha. Pafupipafupi, awiriwo ankapsopsonthana osaonanso kuti mudali ndani m’balamo.

 

Iwo adapitirira kunjoya. Mowa udachucha ngati mgolo wobowoka. Katakwe adali ataledzera pomwe adalandira foniyo.

 

“Bambo a Boyi, Sitayilotu wachita ngozi!” mkazi wake adatero pafonipo.

 

Pakakhala nkhani yovuta mowa umabalalika. “Chani?”

 

“Sitayilo galimoto yamuomba. Moti panopa tili naye ku intensivi ku Central. Mufike mwachangu…”

 

Katakwe adaidula foniyo. Sitayilo adali mwana wake wapamtima. Sadatsanzikenso. Adatuluka m’balamo mutu utazungulira kumusiya Psa Mbalame ali kukamwa yasa ndi kudabwa kuti kwagwanji. Adatenga takisi n’kuthamangira kuchipatala kuja.

 

Adapeza mai ake, mkazi wake ndi abale ake ena atafika kale kuchipatalako. Iye adazizwa aliyense akumuyang’ana modabwa. Adaponya maso uku ndi uku; sadaone chozizwitsa.

 

Ngakhale padali pangozi, mawu a mayi ake ndiwo adamudzidzimutsa, “Kodi achimwene, mwayamba drama?”

 

Funsoli lidamudabwitsa Katakwe. “Bwanji?”

 

“Mukutani m’bulauzi ndi gogoda? Nanga kachipewa kofiyira mwatsomeka kumutuko?”

 

Katakwe adati dzidzidzi-adaiwala kuti adali m’zovala za Psa Mbalame. Mwankhawa dzanja lake lidayenda patsaya pake. Lipisitiki wofiyira adaoneka m’manjamo. Malo ena, nthawi ina, zidakakhala zoseketsa kumuona Katakwe ali mu bulauzi ndi gogoda, kumutu kuli kachipewa kachikazi, lipisitiki wamakisi atapakika m’masaya. Koma ndimomwe idadetserana nkhope ya mkazi wake palibe adaseka. Bata lomwe lidagwa m’chipindamo lidali lowopsa, ngati lija limakhalapo kukakhala kuti kugwa mvula yamkuntho.

 

Aliyense adangoti phe kudikira kuti Katakwe ayankha kuti chiyani!

 

End

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

8 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *