Katakwe Khalidwe la Usatana

Katakwe
Khalidwe la Usatana
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Masiku ano kwadza akuti ‘breaking news’. Aliyense akufuna azikhala woyamba kufalitsa nkhani ikachitika. Izi zikumachitika pamasamba amchezo makamaka pa WhatsApp, pang’ono pa facebook. Ena akumangoponyapo koma ena mpaka akumatsegula timapeji tomwe akutitcha News, Radio kapena TV.

Izi ndi zabwino ndithu. Koma vuto ndilakuti anthu sadziwa kuti utolankhani ndi ntchito yoti munthu umalowa kaye m’kalasi yomwe imakuphuzitsa zofunika kuchita kapena osachita pofalitsa nkhani. Ambiri a mapeji amenewa amakhala mbuli pa utolankhani zotsatira zake amangofalitsa zilizonse ndicholinga chofuna kubeba.

Vutoli likukulanso ndi magulu a pa WhatsApp. Mamembala ambiri a magulu amenewa amakhala ngati kuti bongo alibe. Nkhani imachita kuonekeratu kuti ndiyabodza koma upeza onse akuvomerezana. Pagulu pamatha kuponyedwa chithunzi cholakwika, sungapeze wina wotsutsa, mmalo mwake amapitirira kutumiza zoterezo kumagulu ena otero.

Naye Katakwe sadafune kutsalira. Adatsegula nyuzipepala, wailesi ndi television pa social media. Wailesi ankaitcha Radio Kuswakuswa. Nyuzipepala idali Kung’alula News. Dzina la TV lidali TV Kuphulitsa. Mphekesera ina iliyonse imapezeka waiponya pa social media m’mapeji akewo.

‘Aise, zomwe ukuchitazi n’zosayenera,” mzake Likisho adamulangiza tsiku lina. “Umangofalitsa nkhani zopanda umboni.”

“Pajatu nyuzipepa yanga imangong’alula,” Katakwe adatero. “Kuswakuswa.”

Likisho adagwedeza mutu. “Vuto anthu ena amakhulupirira chili chonse chomwe chimalembedwa pa social media, zoti ambiri omwe mukutumiza ndi anthu ongofuna kutchuka ngati iweyo sadziwa.”

“Zawo zimenezo, ine bola ma ‘like’ pa facebook ndi youtube akuvumbwa. Zinazo ndilibe nazo ntchito.”

“Uyenera kukhala nazo ntchito chifukwa nthawi zina zimabweretsa mpungwe pungwe,” adalangiza Likisho. “Palibe chifukwa choponyera nkhani yoti ulibe nayo umboni pa social media.”

“Aise ndakuuza kuti ine ndimayendera kuswakuswa, uyo chikamuphulikileyo zake.”

Likisho adangoti bola ndanena. Zinthu zimakhala bwino ukamanena za anzako. Koma zikadzakhala zako mpamene umadzamva. Katakwe sadali yekha pa oponya nkhani kapena zithunzi zosakhala bwino pa social media.

Chithunzicho adachiona pa WhatsApp ndipo chimaoneka kuti chazungulira kwambiri. Chidali cha ngozi ya basi yasukulu. Ana ambiri adali atavulala koma mmalo mothandiza ovulalawo anthu ali bize kujambula zithunzi ndi ma video oti aponye pa social media. Sadachedwe adachiponya pa masamba ake amchezo ndi mawu akuti: zangochitika kumene, tikupatsirani zotsatira zake.

Kenaka adaona video yangozi yomweyo. Ndi mtima wozama adazindikira kuti mwana wake adali m’gulu la ana omwe adavulala kwambiri, magazi akutaika koopsa. Munthu wina anali pakalikiliki kujambula video kwinaku akunenera ngati mpira… “palinso mwana uyu yemwe wavulala koopsa ndipo ndimomwe akutaila magazimu ndi zokaikitsa ngati apulumuke…”

Apa mpomwe Katakwe adakumbukira mawu a Likisho. Zimakoma kumaponya zithunzi za ngozi za anthu ena koma tsiku lina zimadzakhala za iwe kapeza za munthu wachibale. Pamenepo mpamene umadzadziwa kuti khalidwe loponya zithunzi zangozi osaganizira kuti abale awo akaona amva bwanji ndi la usatana.

Chifukwa chodzidzimuka, Katakwe adakomoka!

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

3 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *