Katakwe DP Wolemba: Lawrence Kadzitche

Katakwe

DP

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Foni idagwedera. Katakwe adaona kuti idali message ya pa WhatsApp.

 

Idali nambala yachilendo koma ubwino wa WhatsApp, pamakhala chithunzi chija pachingerezi amati Display Picture, DP m’chidule. Pa DP po padali nkhope ya msungwana. Katakwe adamukumbikra mtsikanayo. Adali naye limodzi kusukulu. Panthawiyo ankacheza kwambiri ndipo ankatchulana ‘mahopu”.

 

Uthenga udabwerawo udali chabe moni woti, ‘hello’.

 

‘Hello, mahopu,’ Katakwe adayankha pokumbukira momwe ankachezera kale. ‘Long time!’

 

‘Long time indeed,’ lidabwera yankho.

 

‘Zikutheka?’ adafunsa Katakwe

 

‘Zikutheka. Nanga iweyo?”

 

‘Zilinso bo,” Katakwe adayankha.

 

‘Ndakusowa diya,’ meseji idafika. ‘Tapanga arrange ndikuthireko diso.’

 

Amuna ali ndi vuto. Kaya mwina tisati ali ndi vuto. Mwina tingoti n’chibadidwe chawo. Kuti akane chinthu choti wapempha ndi munthu wamkazi zimawavuta.

 

‘No prob,” adayankha Katakwe podziwa kuti mwayi sudziwika. ‘Tikumane pati?’

 

Msungwanayo adatchula hotela ina yake yotchuka m’taunimo. Adagwirizana zokumana masana atsiku lotsatira.

 

Atafika pa hotelapo, Katakwe anadabwa osaonapo msungwana uja. Kenaka adangomva ‘Hello mahopu’

 

Koma sadali mawu achikazi. Potembenuka adaona adali mnyamata wandevu zidabwera masiku ano zoyala kuzibwano za anyamata ngati carpet.

 

Katakwe adakadzifunsa kuti patse mtedzayo adali ndani, mnyamatayo adapitirira, “Umacheza chani ndi mkazi wanga?”

 

Apa mpomwe Katakwe adatulukira mwachangu kuti buthiyo adali mwamuna wa msungwana adacheza naye uja. Koma nanga zidatheka bwanji iyeyo adziwe?

 

“Amwene, mumacheza naye uja ndine osati mkazi wanga,” khaigoniyo idatero. “Ineyo nambala yanu ndinayipeza mu foni mwake itasevedwa kuti mahopu ndiye pofuna kudziwa kuti mgwirizano wanu ndiwotani nchaka ndimanamizira kuti ndi iyeyo.”

 

“Sorry, amwene, ine pocheza ndimati ndikucheza ndi Melifa,” Katakwe adayankha akutchula dzina la mtsikanayo. “Ndi mzanga wakusukulu. Tili ku sukulu timatchulana mahopu ndiye kuti sanafufute mufonimo.”

 

“Ukuyankhanso mwa mwano?”

 

“Simwano. Inuyo pa DP mudakaika nkhope yanu kuti ndidziwe kuti ndinu. Nkhope ya mkazi wanu imatani pa DP panu?”

 

Zidaoneka kuti funsoli limadamudabwitsa mkuluyo. “Mmesa ndi mkazi wanga?”

 

“Ndiye ife zikutikhudza chani? Anthu mumazikonda zimenezi, kumaika nkhope za akazi anu kaya ana anu pa DP. Pa DP sipoonetsera chikondi kwa akazi anu kapena kushainira kuti muli ndi ana. Zimenezo muziponya pa ma status ngati mukufuna. Pa DP muziyika nkhope zanu tisamavutike kudziwa kuti tikulankhula ndi ndani. Chonchi mudzajiwitsa akazi kwa azinzanu.”

 

End

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

12 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *