Katakwe
Amai, mumaziyamba dala
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Sichikhala chachilendo kuona mwamuna akugulira mkazi wachibwenzi mphatso zosiyanasiyana pomwe kunyumba amangofika chimanjamanja.
Amai ambiri samvetsa chifukwa chomwe amuna awo amagulira zibwenzi mphatso zodula nkumasiya kuchitira zimenezo iwo monga nthiti yovomerezeka. Posapeza yankho, amangoti amuna akakhala ndi chibwenzi amazerezeka.
Komatu sadziwa kuti sikukhalanso kuzerezeka. Vuto limakhala iwowo. Ngati pali mkazi wosayamika, amakhala mkazi wapabanja. Ndiye amuna ambiri saona chifukwa chomagulira mphatso munthu wosayamika.
Katakwe adali pantchito yabwino yomwe inkamuyendetsa mpaka kumayiko akunja. Nthawi zonse akapita kunjako samalephera kugula mphatso yoti akapatse mkazi wake.
Vuto limakhala loti maso a mwamuna ndi a mkazi amasiyana maonedwe. Nthawi zonse Katakwe akagula mphatso yokapatsa mkazi wakeyo, yankho linkakhala lokhumudwitsa.
“Moti mu London monse munaona kuti dilesi lobeba ndi limeneli?” mkazi wake amafunsa. “Mukufuna anthu azindiyesa chidole kapena hule?”
Chonsechotu 100 dollars idali yoti yapita pa dilesilo!
Mwina ngati inali nsapato, “He he he, nsapatoyi muti ndikavala ndizingokhala ngati ndakwera pa mtondo!” Heh, nsapatotu yoti iye adagula 1,500 rands ku Johannesburg.
Kaya magalasi amanyado akuda a mmaso, “Mukufuna ndizioneka ngati kadzidzi ndi vimagalasi vodzaza kumaso mwagulavi?”
Chilichonse ankachipezera chifukwa. ‘Eh, dilesi limeneli ndalama zonsenzo? Iii zimenezi zidatuluka mufashoni! Mtundu umenewu anthu azindiyesea wa staniki?’
Mwana wamwamuna adakatani? Kusiya basi. Powawidwa Katakwe adapeza kachibwenzi. Inu, akangobwera ndi dilesi olo la pakaunjika kumakhala kuthokoza. Nanji agule chinthu chodula, ‘zikomo, yewo, tutogolere, asante, thanks, merci, danke, gracias, obrigado’ wake amakhala woombera mmanja nkuphazi- honey darling, sweetheart akuchekenira!
Eetu, nkhani ndi imeneyo!
End
????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????tutogorele
kkkkk