Katakwe ZINA ZIKACHITIKA

Katakwe

ZINA ZIKACHITIKA

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Anthu ambiri amagwa mmavuto osati chifukwa choti alakwitsa koma chifukwa choti zina zake zachitika zomwe ngakhale atafotokoza bwanji, palibe yemwe angakhulupirire.

 

Ngati muli pabanja, dzayeseni kukhala pa WhatsApp nkumacheza ndi mzanu, mkazi wanu ali pomwepo. Dzasekeni kapena kumwetulira pa zomwe mukucheza ndi mzanuzo, nokha mudzaona momwe nkhope ya mwana wamkazi idzasinthire. Kupanda kuzitenga bwino mpaka nkhani imeneyo idzathera kwa ankhoswe.

 

Mukhoza kuti mutha kufotokoza chomwe chikukupangitsani kuseka kapena kumwetulira. Komatu zomwe munthu wamwamuna angaone ngati zoseketsa mzimayi sangaonepo choti n’kuseka. Nde olo mudzamuonetse adzakuuzani kuti mukunama, sizomwe mumaseka, mwafufuta.

 

Chabwino. Tsikulo Katakwe adapita kumsonkhano womwe kampani yomwe amagwirako ntchito idapangitsa ku Mangochi. Monga mumadziwa, azimai amakonda kwambiri kujambulitsa zithunzi. Mmodzi mwa asungwana omwe amagwira nawo ntchito limodzi adamupempha Katakwe kuti amutoleko zithunzi.

 

Katakwe adatenga foni yake ndikujambula zithunzi zinayi zomwe msungwanayo adaphoza mmbali mwa nyanja. Msonkhano utatha, Katakwe adatumiza zithunzi zija kwa msungwanayo iye n’kunyamuka ulendo wobwerera kunyumba.

 

Kuti zinthu sizili bwino, atangofika, adaonera nkhope ya mkazi wake; idali yokwiya kuposa yagalu wolusa.

 

“Mumazemba, lero ndakugwirani,” mwana wamkazi adamulandira ndi mulandu.

 

“Mwandigwira?” Katakwe adafunsa modabwa.

 

“Eya. Zithunzi za msungwana zikutani pa status yako?”

 

Katakwe adati dzidzidzi. Adatulutsa foni yake. Zithunzi za msungwana uja zidalidi pa status yake ya WhatsApp. Apa mpomwe adazindikira kuti mmalo motumizira msungwana uja, zithunzi zija adziponya mwangozi pa status pake.

 

“Pepani, make mwana. Msungwanayu ndimagwira naye ntchito limodzi ndiye anandipempha kuti ndimujambuleko,” Katakwe adafotokoza chilungamo. “Koma mmalo momutumizira ndiye kuti ndatumiza mwangozi pa status panga.”

 

“Msungwanayu wanyamula foni mmanja mwake, bwanji sunajambulire yakeyo?” Katakwe adalandira funso.

 

“Ndatitu zinali zoti nditumizire iyeyo…”

 

Mkazi wake adamudula pokweza dzanja. “Nkhani yoti mwatumiza mwangozi ikumveka. Koma nkhani ili poti; zithunzizi zikupezeka bwanji mufoni mwanu? Nkhani imeneyitu ikukafika kwa ankhoswe.”

 

“Chabwino timuyimbire kuti afotokoze yekha,” Katakwe adapereka ganizo.

 

Mwana wamkazi adaseka monyodola. “Ndiye angavomere kuti muli pachibwenzi? Katakwe, I am not stupid.”

 

Katakwe adadziwa kuti olo adakafotokoza bwanji sizidakamveka. Adapemphedwa kuti ajambule zithunzi ndipo iye adajambula popanda maganizo ena ali onse oipa. Koma mkazi wake adakakhulupirira bwanji?

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

3 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *