Katakwe ATAMBWALI SAMETANA

Katakwe
ATAMBWALI SAMETANA
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Ngakhale sadaonetsere, malume ndi zakhali a Katakwewo adachoka pakhomopo mokhumudwa.

“Apa ndiye tathana nawo basi,” Katakwe adanyadira.

“Sukunama,” mkazi wake adavomereza. “Malume ako adamkwitsa dyera.”

“Osati iwo wokha aja. Ndi zakhali omwe,” adatero Katakwe.

Mkazi wa Katakwe adaseka. “Tsono umati anthu oti adakwatirana pachisuweni n’kusiyana zochita bwanji?”

Nkhanitu apa idali ya tiyi kaya titi mtentha ndevu. Malume a Katakwe, a Topitopi, ndi zakhali ake a Namnyama sankatha phazi pakhomopo. Vuto silidali kubwerako koma mamwedwe awo a tiyi. Awiriwa ankakonda tiyi kwambiri. Akafika ankatha shuga ndi mkaka wonse omwe amapatsidwa.

Katakwe ndi mkazi wake atadya mutu adaganiza zochenjerera awiriwo. Iwo adagula timakapu tating’onoting’ono kwambiri.

“Kuti amalize paketi yashuga azichita kufunika kumwa makapu khumi,” Katakwe adatafula.

“Kodi ngati mpata umenewo aziupezanso? Monga ndinachitira apapa, ndizingoti akathira kapu imodzi ine basi n’kuchotsa madzi kunamizira kuti ndimaona ngati samwanso wina,” adatero mkazi wake.

“Apa taitha,” adabwekera Katakwe. “Zinthu zadula; tiyi azichita kumwa ngati auzidwa kuti aphedwa akapanda kumaliza shuga ndi mkaka?”

“Apa mwaing’alula, dadi,” adathirira mang’ombe mkazi wake. “Apezana ndi atambwali.”

Sabata yotsatira, a Topitopi adafikanso limodzi ndi a Namnyama. Mkazi wa Katakwe adabweretsa zonse zofunikira kumwa tiyi; buledi, madzi otentha ambiri, shuga, ndi mkaka. Pobwereka kulankhula kwa andale zonsezi zidali ngambwingambwi koma timakapu tidali tating’ono ngati zidole.

“Malume, zakhali, titenthetsetu kukhosi,” Katakwe adapereka kalibu. “Pepani monga munaonera sabata yatha makapu mudawazolowera aja adasweka ndiye muzimwera anyuwaniwa.”

A Topitopi ndi zakhaliwo adayang’anitsitsana. Onse adamwetulira.

“Osadandaula, mphwanga,” a Topitopi adatero akupisa mkati mwa jasi lomwe adavala. “Pano ndayamba kuyenda mokonzeka.”

Katakwe anadabwa malume akewo akutulutsa chikapu chachikulu cha pulasitiki chija ena amachitcha msonkho ukhale. “Ndaona kuti m’tauni muno khalidwe lokhala ndi timakapu tating’ono likuchuluka ndiye ndagogula yanga yomwe ndiziyenda nayo.”

Katakwe adakadabwa, nawonso zakhali adatulutsa chawo chikapu chapulasitiki m’chikwama chawo. “Nanenso ndagula yanga.”

Makapu awiri okhawo adakwanitsa kumaliza shuga ndi mkaka wonse. Apa mpamene Katakwe ndi mkazi wake adakumbukira kuti atambwali sametana.

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *