Katakwe AKUMANA NDI GULANKUMWERE

Katakwe

AKUMANA NDI GULANKUMWERE

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Mudali mu bala ija yotchuka ya mu Devil Street. Katakwe adakhala pakona ndi Likisho akumwa mowa, kwinaku akutsuka maso powona asungwana wokopa alendo omwe ankayendayenda movinitsa mbuyo pofuna kupeza makasitomala.

 

Kenaka mu balamo mudalowa mkulu wina. Adali wamtali ndi woonda. Mutu wake udali waukulu chipumi n’kumapita ukuchepa mpaka kukasongoka pofika pachigama. Timaso take tidali tating’ono ndi towala ngati tankhuku. Nkhopeyo inkangooneka ngati ya nkhandwe. Ngakhale adali wochepa thupi, mimba yake idali yofufuma ngati mpira.

 

Mkuluyo adali mu bulandi lothimbirira ndi buluku lolekeza mu akatumba. Kuphazi kudali masilipazi.

 

“Barman, tawerengetsa uli ndi mowa wa ndalama zingati mu filiji,” adatero mokuwa mkuluyo akuyika waleti yodzimbidwa ndi ndalama pa kauntala.

 

“Aise, sindikukaika, mkulu uyo ndi m’chikumbe,” adatero Katakwe motsika.

 

“Zachidziwikire,” adavomereza Likisho. “Paja achikumbe amatero akasanja.”

 

“Ndalama zili mu wallet yo zikhoza kugula mowa onse muno.”

 

Katakwe adadya mutu mwachangu. “Aise, titachenjera manja, mkulu ameneyu akhoza kutisambitsa bawa lero.”

 

Awiriwo adagundana mitu ndipo posakhalitsa adagwirizana chochita. Iwo adamuyitana mkulu uja. “Madala, khalani pano tidzimwera limodzi,” adatero Katakwe. “Mukumwa chiyani?”

 

“Girini,” adayankha mkuluyo.

 

“Barman, bigiwa tawabweretsera mabotolo anayi a girini,” adatero Katakwe. Adatembenukira kwa mnyamata wootcha nyama. “Aise, bwanawa uwaotchere nyama momwe angafunire.”

 

Apo iwo adayamba kumwa uku nkhani zikuphulika. Mkuluyo adati dzina lake lidali Dazibomu, ndipo kwawo kudali ku Kasungu.

 

“Najagulitsha fodya ku okoshoni ndiye nilifuna nikonjweko,” adalengeza Dazibomu m’chichewa cha ku Kasungu.

 

Kumva choncho, Katakwe adagula mowa molimba mtima kuti mkuluyo akaledzera, awagulire mowa mowolowa manja.

 

“Tsano onyamata inu nufuna lero musambe mowa,” adatero Dazibomu akuyimilira. “Dikirani nimuuze Barman akubweretchereni makeleti osanu.”

 

Iye adapita pa kauntala pomwe adalankhula ndi Barman kwinaku akupanga chizindikiro ndizala zake choonetsa faifi, kenaka n’kuloza pomwe padali Katakwe ndi Likisho. Atatero adatuluka ngati akukataya madzi.

 

Katakwe ndi Likisho anadabwa nthawi ikupita barman uja osabweretsa mowa. Ngakhale mkulu uja sadabwerenso. Poti ndalama zidali zitawathera, iwo adaganiza zomufunsa barman uja.

 

“Amwene, mowa anayitanitsa mchikumbe uja uli kuti?” adafunsa Katakwe.

 

Barman adaseka. “Mchikumbe uti? Uja mumamwa naye mowa uja timangomutcha Gulankumwere. Ndi dolo la m’tawuni momwe muno lomwe limanamizira kuti ndi mchikumbe kuti lizimwera mowa anthu otengeka.”

 

“Ndiye muja anabwera pakauntala pano nkumaonetsa ngati akuitanitsa mowa amati chani?” Katakwe ndi Likisho adafuna kudziwa.

 

Wogulitsa mowayo adasekanso. “Amanditsanzika. Muja amaloza inu muja amati mumafuna kugula mowa usanu koma mubwera nokha kudzayitanitsa.”

 

Mochedwa, Katakwe ndi Likisho adazindikira kuti ayendedwa njomba. Onse adangoti ‘Aaaaaaaah!”

 

Nthawi yomweyo mnyamata wootcha nyama uja adatulukira. “Paja munati mkulu uja azingoitanitsa nyama momwe angafunire . Popita watenga ya 10 pin yoti akadye ndi ana kunyumba.”

 

END

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

1 Comment

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *