Katakwe ZIKHULUPIRIRO

Katakwe
ZIKHULUPIRIRO
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Mwana ndi yemwe adadzamutenga Katakwe. “Adadi, anthutu akufuna kuwaotcha anzanu!” mwanayo adafuwula mwankhawa.

Katakwe adasiya zomwe ankachita nkuthamangira komwe amaloza mwanayo. Kumeneko adapeza khamu la anthu litasonkhana. Iye adalowa mkati mwa khwimbilo ndipo zomwe adaona zidamuopsa. Likisho adali atamangidwa nyakula ndipo nkhope idali itatupa ngati walumidwa ndi njuchi zolusa.

Malume ake a Topitopi ndiwo amatsogolera gululo, akujiya mozungulira mzakeyo nsakali ili mmanja.

“Ngati suwulula basi tikuotcha,” iwo adaopseza.

“Malume, chikuchitika nchiyani?” Katakwe adafunsa.

“Maliro tayika dzana aja; mfiti tayipeza,” adayankha a Topitopi.

Katakwe adawayang’ana malume akewo modabwa. “Mwapeza mfiti? Mmayesa Dubiyasi adamwalira atagwa mumtengo?”

“Dubiyasi wakhala zaka zingati akukwera mumtengo kukasadza nthambi?” a Topitopi adayankha ndi funso.

“Zaka zoposa khumi,” adayankha Katakwe.

“Mzaka zonsezo, adagwako?”

Katakwe adaluka nsidze. “Ayi.”

“Ndiye zitheka bwanji kuti ulendo uno wokha agwe, komanso osangoti kugwa kokha komanso mpaka kumwalira?”

Katakwe adaseka ngati zabwino. “Malume, mukufunsa funso limenelo ndinu? Imeneyi ndingozi. Aliyense akhoza kuchita ngozi…”

“Dubiyasi adali katswiri…”

“Malume, kodi mumati Dubiyasi azigwa tsiku lililonse mumtengomo kuti mukhulupirire kuti ndingozi?”

A Topitopi adati jenkha. “Pajatu chaka chatha ankalimbirana munda…”

“Anthu amakangana kumene koma zina zimachita kuonekeratu kuti ndi ngozi…”

“Dubiyasi adali katswiri pantchito yake yosadza mitengo…”

“Malume, munthu amachita ngozi pantchito yake kumene. Msodzi amatha kumira panyanja. Dilaiva kufera pamsewu…ndiye ngoziyo. Munthu woti salowa mmadzi sangafere mmadzi.”

“Ayi, mwana ameneyu wakakata nabo umfiti. Chaka icho ndi uja tidayika mchemwali wake.”

“Malume, vuto lathu anthufe ndi limenelo. Sitifuna kuvomereza kuti munthu akhoza kufa chabe, timafuna mpaka timugwire wina umfiti. Munthu angogwa, timati wakhomedwa hamala kuiwala kuti kuli matenda ena omwe amatha kupha munthu mopanda odi. Adwale nthawi yaitali timati wina wamuponyera matenda osachizika,” Katakwe adaunikira. “Munthu akafa tiyeni tivomereze kuti panthawi yake aliyense adzafa mnjira iyi kapena iyo koma tisamalowetsepo umfiti. Timangodana ndi zikhulipiriro zabodza.”

“Komabe ngozi zina zimadabwitsa…”

Katakwe adawadula tsibweni akewo pokweza dzanja. “Ngozi imayenera kudabwitsa kumene chifukwa sichikhala chinthu chokonzekera. Nthawi zina galimoto imakapezeka itapachikika mumtengo anthu nkumati zatheka bwanji!”

“Nde umfitibo bumenebo…”

Katakwe adagwedeza mutu. “Chomvetsa chisoni chimakhala chakuti ngakhale anthu ophunzira amene amakhulupirira zimenezi. Monga inuyo a Topitopi ndinu munthu wozindikira, mwakhala ku Kabwe, Sozibele ndi Jubeki, ndithu nkumaona kuti sizingatheke munthu kugwa mumtengo mwangozi?”

End.

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

6 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *