Mgodi Uvuta

Akafika kumabala a ku Chingwirizano, mahule amadziwa kuti tsikulo kuli kusamba mowa komanso ndalama yapadera siyilephera kupezeka. Motero, iwo adamupatsa dzina lakuti Walodi Banki. Dzinalitu  lidachokera ku bungwe lija la zachuma padziko lonse lomwe pachingerezi amalitcha World Bank.

“A Walodi Banki, lero mukuti bwanji?” Yaliyali, hule lodziwa kudyera amuna, linkatero iye akangotulukira.

“Zakumwa ndi your choice.  Tafika ife a mponda matambala.”

Akatero namwaliyo ankazunguza maso ake akuluakulu oyang’ana moleza. “Nanga nkhaniyo?”

“Ifetu timapereka ten times the usual charge.”

Munthutu ankatchedwa Walodi Bankiyu, akafika ku Area 3 adali ndi dzina lina. Katakwe. Uku adali munthu wabanja lake ndipo adali ndi ana asanu. Adalinso pantchito yabwino koma chifukwa chomwaza ndalama mosaganizira, pakhomo pake padali pausiwa woopsa. Kuwona ulombo womwe udali panyumba pakepo, padali povuta kuganizira kuti iyeyu kumabala ankakhala chikhwaya.

Mkazi wake akamufunsa komwe kumapita ndalama, Katakwe amangopereka mayankho osamveka bwino. Mkaziyo akati afunsitse, iye amangoyamba kukalipa.

“Nanga zomwera mowa deile mumazitenga kuti?”

“Amandimwetsa anzanga,” iye ankayankha mosasamala.

Munthu wamayi adawona kuti apa amayendedwa njomba. Mwamuna wakeyo amachita kupambana chiyani kuti anthu azimumwetsa tsiku lili lonse?

Chimaphikitsa nsima ndi njala. Mwana wamkazi atagona nayo kwa masiku angapo, adaganiza zolondola mwamuna wake kumowa komweko.

Adakamupeza Katakwe ku Chigwirizano mu bala ija amati Dyeratu Kuli Edzi. “Komatu anthu ndiye mukuupeza,” adatero mkazi wakeyo akumwaza maso ake pamabotolo omwe adamuzungulira Katakwe. “Kuyala mowa chomwechi ngati muli paphwando!”

“Ujeni….ndiye kuti…andi…andigulira anzanga…komanso enawa sianga,” Katakwe adachita chibwibwi, mumtima akupemphera kuti hule lomwe amamwa nalo limodzi lisatulukire msanga kuchokera kokataya madzi.

Koma sizidatero. Yaliyali adatulukira, ali m’siketi yosiya ntchafu zonse pamtunda. Mawere ofufuma ngati mapapaya adafuna kuphulitsa bulauzi yothina ngati sokosi yomwenso inkaonetsa mchombo. Pamchombopo padajambulidwa njoka ya mtundu wa mamba itadzutsa mutu.

Hulelo lidangofikira kuima kumanso kwa mkazi wa Katakwe n’kukoka tsinya. “Chikatere?”

Mkazi wa Katakwe anadabwa. “Bwanji?”

“Asisi, mwakwera yodzadza,” adasimbwa Yaliyali manja ali m’chiuno, “Tsikani.”

“Ukutanthauza chiani?” adafunsa mokwiya mkazi wa Katakwe.

Yaliyali adazunguza maso ake akuluakulu kenaka nkuseka. “Mgodi mukufuna kujiyawu ndiwanga ndipo zonse tagwirizana kale.” Iye adapisa m’thumba natulutsamo ma K500 angapo. “Ya ku rumu ndi iyi wandipatsa kale. Pano mungotaya nthawi; kafuneni msika wina.”

Mtima wa mkazi wa Katakwe udadumpha. “Chani? Ukutanthauza kuti ndalama zonsenzi wakupatsa ndi iyeyu?”

Yaliyali adasekanso. “Izinso n’chabe; akati wasanja timadya money. Timagwira ma ten pin osaphatikizapo za beer pamenepo. Umati timamutchuliranji World Bank?

Katakwe adadziwiratu kuti monga adachitira Delila m’Buku Lopatulika, hulelo lidali litamupereka kwa afirisiti monga Samisoni!

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *