Katakwe Pamsewu

Kwa omwe simudziwa, ngati munthu ukupita ku Lilongwe kuchoka ku Blantyre, pali malo ena pafupi ndi Kameza Roundabout pomwe anthu amakwerera matola opita ku Lilongwe. Katakwe adamutenga mnyamatayo pamenepo.

Adali mnyamata wazaka zopitirira makumi awiri ndipo adavala thalauza lokhwefula ndi malaya othina. Monga momwe achinyamata amasiku ano akupangira, ndevu zidayala kuchigama ngati udzu. “Thanks, brother,” mnyamatayo adathokoza akukwera. “Lero mathilansipoti avuta, magalimoto sakuima.”

Apo ulendo udapsa. Katakwe adaponya nyimbo ya Lawrence Mbenjere yomwe ankaigomera. Ndinkati udzavala kamisolo yoyendera limoti, anawa adzavala mikuna yoyendera mabatele

Kenaka adangomva nyimbo ija ziii. Poyangana adaona kuti adazimitsa ndi mnyamata uja. “Amwene, mulibe nyimbo ya Diamond Platinumz ija amati Waah?” Katakwe anadabwa ndi funsoli. Asadayankhe mnyamatayo adafunsanso, “Kapena . Ya Kiss Daniel?”

“Ndilibe,” Katakwe adayankha akumuyang ana mnyamatayo modabwa.

“No prob,” adatero mnyamatayo akautulutsa foni yake. “Ndili nazo mu fonimu, tilumikiza pa Bluetooth.”

Zidatheka ndipo posachedwa Kiss Daniel adatibuka. “Lemme see you go low low low, Buga won…Izi nde nyimbo,” adabwekera mnyamatayo akukweza volume. “Osati za adzimwa munaika zija.”

Katakwe adafuna kulankhula koma kenaka adaganiza zongomata pakamwa. Ulendo udapitirira. Akuyandikira pa Lirangwe, galimoto ya mtundu wa Audi idawadutsa. “Four rings amwene, makina omwe amayendera Transporter mu filimu,” adayamikira mnyamata uja.

Mmalo moyankhirapo, Katakwe adangomuponyera diso mnyamatayo. Akudutsa pa Mdeka, galimoto ya mtundu wa Toyota Fortuner idawadutsa. “Awanso nde makina eni eni, katundumadzi, 2 hours kukafika ku Lilongwe.”

Ulendo uno Katakwe adayankhirapo. “Mwatero, achimwene?” Asadayankhe mnyamatayo, Toyota VX idawapanganso overtake. “Awa nde mashini mapeto. Ndege yapansi, sizinazi.”

“Zinazi ndi chani?”

Mnyamatayo adaseka. “Manyaka. Zinazi ndizongofunika kumakagulira ndiwo kumsika osati kuthera mtunda. Kukafika ku Lilongwe 10 hours!”

Katakwe adaponda buleki ndikuima pambali pa msewu. “Achimwene, tsikani galimoto ino.”

Mnyamata uja adadzidzimuka. “Bwanji, brother?”

“Ndalephera kukupirirani. Mwayambira kusintha nyimbo mwati zanga ndi za azimwale. Galimoto ikatipanga overtake muli ee awa nde mashini, ee mwakuti Nde poti ino sigalimoto tsikani, mukakwere makina mukukhumbirawo.”

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *