Kunja Kwa Corona

KUNJA NKWA CORONA
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Lidali dera lachilendo koma Katakwe ndi mkazi wake adapitako kukaona mzawo yemwe adasamukira mbali imeneyo. Adazindikira kuti kumeneko kudalibe magalimoto a matola ndipo njira yokhayo yoyendera idali kudzera mnjinga zamoto za kabaza.

Pamalo a kabazawo adapeza njinga imodzi. Katakwe adaganiza zoti wanjingayo akasiye kaye mkazi wake kenako adzamutenge iyeyo.

“Chemwali, awa ndi mashini kawawa, tiyeni kwerani,” adatero wakabazayo mwamatama.

Mkazi wa Katakwe adakwera nakhala momutalikira pang’ono wakabazayo.

“Mai, mthuthuthu uno ndi ndege yapansi, senderani kuno,” wakabazayo adalamula.

Mkazi wa Katakwe adasendera. “Good,” adabwekera wanjingayo. “Sister, njinga sichinthu chosewera nacho. Ndikumbatireni, ine sindifuna zangozi.”

Mkazi wa Katakwe adachita monga adauzidwira ndipo ulendo udapsa. Katakwe sadalankhulepo. Adangoti ntchito iliyonse ili ndi malamulo ake.

Patapita kanthawi wakabaza uja adatulukira kudzatenga Katakwe.

“Mwaonatu achimwene, njinga iyi ndi Rolls Royce. No breakdown,” adadzitamirira wa kabazayo.

“Ndaonadi,” Katakwe adavomereza.

Pokumbukira malangizo adapereka kwa mkazi wake uja pokwera njinga ija, naye Katakwe adamukumbatira wakabazayo. Koma mawu adalandira adamudzidzimutsa.

“Eeh , mdala bwanji? Ndiwe gay?”

“Bwanji?”

“Njinga nchinthu choopsa. Sukuona kukutentha? Sendera kumbuyo ugwire keliyala ndiziyendetsa njinga momasuka.”

Katakwe adangoti kakasi.

“Komanso sukuona kunja nkwa korona nde uzindipumiranso pafupi?”

End

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *