KULIMBITSA THUPI

Katakwe
KULIMBITSA THUPI
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Amai ena sasiyana ndi mwana. Amati akafuna kanthu, mwamuna wawo nkuwakanira, amakunyuka ngati muja amachitira mwana wotumbwa. Mtundu wa amai akhalidwe lotere ndi aja amapangitsa amuna awo mpaka kukaba kuntchito pofuna kuwasangalatsa.

Mkazi wa Katakwe adali mgulu la amai woterewa. Akafuna chinthu amachilimbikira mpaka apatsidwe. Katakwe akakana amatha masiku osalankhulana ngakhale nkuchipinda komwe. Pofuna kubweretsa mtendere, Katakwe amangogonja.

Nkhani yomwe idavuta ulendo uno idali yomwe yatchuka masiku anoyi-yolimbitsa thupi. “Ndikufuna nane mukandilipirire ku jimu,” Nabetha adatero.

“Make mwana, mukudziwa panopa ndalama zativuta, ndiye mungamakambe za ku gym?” adafunsa Katakwe.

“Poti ndalama zavuta ndiye mukufuna ndife ndi BP kuti mukwatire mkazi wotchipa?” adafunsa mwana wamkazi mwamwano.

Katakwe adapuma mozama. “Sindikutero. Mmalo mopita ku gym mukhoza kumakayenda kapena kuthamanga kumsewu. Thupi lizilimba koma mosaboola mthumba.”

“Hede!” adaseka monyodola Nabetha akuomba mmanja. “Ineyo, Nabetha, ndizikathamanga kumsewu anzanga akunjoya ku jimu! Ndiyenso sindinenso mwana wa a Bethatu!”

Pongofuna kutha nkhani, Katakwe adavomera. Adapita kukalipira ku gym ina yodula m’tauni. Nabetha adayamba kumapita ku jimuko. Mathero a sabata imeneyo wantchito wawo adachoka. Katakwe, Nabetha ndi ana awo ndi amene adatsala pakhomopo.

Ndiyetu ana ndi bambo awo adazigwira. Anna, tandipatsirako madzi akumwa. Tandipatsirako limoti, Jemu. Tasunthaniko mpandowo, bambo. Uyutu adali mkazi wake kulamula atangokhala pa sofa.

Katakwe sadathe kumvetsa. Izi adali atazionanso mmakomo ambiri. Padali amai ambiri omwe amapita ku ma gym kapena kukathamanga kuti alimbitse thupi. Chonsecho akafika pakhomo samafuna kugwira ntchito ina iliyonse. Kodi adakamagwira ntchito olo chabwino osagwira ntchito poti ndi akazi amabwana koma adakamayenda kumakadzitungira madzi akumwa, kukatenga okha limoti ya TV olo kukatenga chinthu akachifuna, zimenezi sizidakakhala zokwanira kulimbitsa thupi?

Adafuna kuti amulankhule mkazi wakeyo koma adadziwa kuti yankho lake silikhala logwirizana ndi nkhaniyo koma kungokhadzula kuti ngati mwatopa nkundilipirira ku jimu bwanji osangonena?
End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *