Mchenga Woyera

Katakwe

Mchenga Woyera

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Sabata yonseyo, Katakwe adakhala akutafuna gondolosi, kubwira chiswa ndi kumwa mthibulo womwe adaoda kwa mzimayi uja amagulitsa muti woterewu pafupi ndi banki ija ya ku City Centre. Monga momwe adamufotokozera mzake Likisho, iye amachita izi kukonzekera kufika kwa bwenzi lake Sweet Maria.

 

“Man, panopa ndine mashini, AK47 mfuti yosajama ngakhale mmadzi,” iye adabwekera kwa Likisho akunyamuka kukamuchingamira Sweet Maria ku siteji ya basi. “Lero ndifera pomwe ndidachoka!”

 

Komatu sikuti Katakwe adali ataonanapo maso ndi maso ndi bwenzi lakelo. Ayi. Ubwenzi wake ndi Sweet Maria udayamba kudzera pa facebook. Katakwe adatengeka ndi zithunzi zomwe namwaliyo ankaika pa facebook.

 

Pa asungwana onse omwe adawaona pa facebook, mkazi yemwe adamugwira mtima adali Sweet Maria. Adali wamsinkhu wapakatikati, wonenepera ndi woyera kwambiri. Nkhope yake yonga mtima idali yosalala ngati khungu la khanda. Mwana wamkazi adali ndi thupi loumbidwa ngati la fulufute lalikazi-mawere a njo ngati tizulu, chiuno nkudzaning’a kenaka ntchafu nkudzavwandamuka. Mzithunzizo ankavala zovala zothina ndipo Katakwe adatha kuona mbuyo ija agule amati yoswa mtondo.

 

Maso ndi mtima wa Katakwe udakhutira ndi buthulo. Zaka za Katakwe zimathamangira makumi atatu. Namwaliyo amaoneka kamsungwana kosadutsa zaka makumi awiri.

 

Katakwe sadachedwe. Adamulembera Sweet Maria ku inbox kuti wagwa naye m’chikondi. Naye namwali adati zikhale chomwecho. Apotu chikondi cha pa facebook chidakula ngati bowa. Mwana wamkazi ankamutumizira Katakwe zithunzi zokhetsa dovu.

 

“Darling Sweet Maria, ubwere kuno ine ndatopa n’kutsuka mapoto,” Katakwe adamuyitana namwaliyo. “Ngati sivuto kwa iwe tidzangolowana zina zonse tidzapanga tili m’banja.”

 

Sweet Maria adayankha kuti banja ndi anthu awiri ndipo iye amabwera kudzakhala ngakhale popanda ankhoswe. Apatu mpomwe Katakwe adayambira kumwa mthibulo, mkwapukwapu, nganganga ndi mtera wina wotero.

 

Basi yochoka ku Blantyre yomwe Anna Maria adati akwera itafika, Katakwe anadabwa kuti anthu onse atsika popanda getsi lomuthobwa. Nyenyezi yakeyo idali kuti? Kapena idangofuna kumudyera ya thilansipoti?

 

Adakadzifunsa izi adangozindikira akutembenuzidwa ndipo akupsopsonedwa pamlomo ndi mmasaya ndi mayi wina wake wachilendo. Katakwe adangoyima njo ngati wauma, akudabwa kuti ndani amamupatsa chikondi chachizungucho.

 

“Heh, nawenso moti sukundizindikira?” adafunsa mkaziyo modabwa.

 

Katakwe adamuyang’ana mayiyo. Adali woti kumaso adapsa chifukwa chodzola mankhwala oyeretsa. Ziphuphu zidali lakata ngati mikanda yomwazika. Ngakhale zaka zakenso zimaonekeratu zidali zoposa za Katakwe. Sadalinso ndi ma hip olo mbuyo yoswa mtondo adatengeka nayo ija. Shape yonse ija idali ya bodza. Zithunzi zija zidali zija pachingerezi amati zopanga photoshop.

 

“Ndine Sweet Maria!”

 

Mukadakhala mu filimu, Katakwe adakakomoka ndi kudabwa. Koma apa adangoti kukamwa yasa, maso atatuzula ngati akuona mzukwa.

 

Zithunzi zija zidamunamiza. Ntchembereyo inkamutumizira zithunzi zojudula. Ndipo iye monga Madoli mmwambi wa akulu akale, adafera mchenga wiyera!

 

End

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *