Awona Malodza

 

Katakwe

Awona malodza

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Mukadzawona malonda akuyalidwa tsiku lilonse ndiye kuti amagulidwa. Katundu wosayenda malonda amachotsedwa pamsika.

 

Motero, mukamayenda usiku n’kuwona asungwana ovala mosasiyana n’kukhala maliseche atayima mmbali mwa msewu musamadabwe kuti amawatenga ndi ndani. Ndi anthu oyenda pagalimoto ngati inuyo. Adakakhala kuti satengedwa sadakalola kumauma ndi chisanu usiku.

 

Katakwe adali mmodzi mwa anthu omwe amatenga asungwana amenewa. Amati akamutenga msungwana, amakacheza naye pa resitihausi ina yake kwa Kudya.

 

Komatu sikuti Katakwe adali pamphala. Iye adali wachikulire ndithu ndi wapabanja labwinobwino. Mwana wake woyamba adali buthu ndithu lomwe limakhala ku Naperi ndi asungwana anzake kwinaku akufuna ntchito. Kuntchito Katakwe adali ndi udindo wabwino. Kutchalitchi adali mkulu wampingo wodalilika.

 

Komabe poti mdima umabisa, iye amatha kumachita ntchito za mu mdima popanda aliyense kudziwa. Pofuna kuti asamadziwike, akadziwa kuti akatenga msungwana, iye amabwereka galimoto ya anzake. Amavalanso chipewa kuti womudziwa atamuona asamuzindikire.

 

Lidali tsiku lachisanu. Kamdima katagwa, iye adaganiza zokatenga kamsoti pamalo paja pamayima asungwana usiku pa a Kamba kuti akachite nako masewera a tambala ndi msoti. Adabwereka galimoto ya mzake Dakwani ponamizira kuti yake ikuvuta. Adadzikuta mjekete lija amati sintopola nakweza kolala. Kenaka adavala chipewa chachikulu chija chimakhala ndi ma dread oluka ndipo wovala amaoneka ngati Rasta wa ma dread, mmaso n’kuponyamo magalasi.

 

“Hahaha, apa mani ali mu camouflage, palibe angandizindikire, iye adanyadira akudziyangna pagalasi la galimotoyo.

 

Atayimitsa galimoto, asungwana adakhamukira kugalimoto yakeyo. Nawonso asungwana oyenda usiku amadzibisa kuti akamayenda masana anthu asamawazindikire. Usiku amakhala atavala zovala zogwirizana ndi ntchito yawoyo.

 

Padali asungwana amtundu wonse-aatali, aafupi, onenepa, owonda, oyera, akudaPokhala munthu woti akufuna kudzibisa, adalibe danga loti achite kuyanganitsitsa. Adaloza mmodzi mwa asungwanawo.

 

Pofunabe kuti ngati anthu angamuwone azingoti wamupatsa lift msungwanayo, iye adaliuza hulelo kuti likhale mpando wammbuyo. Ulendo wosalankhulana udapsa. Iwo adakalowa mwachangu murumu yomwe Katakwe adabukiratu kwa a Kudya.

 

Munthu ukhoza kudzibisa koma paja nkhaniyo ili ngati kutamba; mfiti siyitamba m’zovala. Katakwe atavula zovala mpomwe anadabwa namwali uja akukuwa, Adadi!

 

Naye poyangana, mpomwe adazindikira kuti msungwana yemwe adadziphoda mozira ngati namalocha, atavala kasiketi kowoneta panti, mchombo uli pamtunda, adali mwana wake-

 

Flora! iye adakuwa akuyangana chinkhanira chomwe mwana wakeyo adajambula pakati pa mawere ake!

 

End

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

3 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *