Zochitika pa Khirisimasi

Katakwe

ZOCHITIKA PA KHIRISIMASI

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Pachingerezi amati Christmas Eve. Pachichewa timangoti pa 24 December, tsiku loti mawa ndi khrisimasi. Likisho adatulukira pakhomo pa Katakwe cha ku mmawa.

 

“Aise ukuti nayo bwanji khrisimasi ya chaka chino?” adafunsa Likisho yemwe amafuna Katakwe amudyetse khrisimasi.

 

“Inetu khrisimasi n’kadyera patali; moti unowu ngwakunyanja,” Katakwe adayankha. “Ndufuna ndizikapsontha beer miyendo ili mmadzi ngati tourist. Now watch this,” iye adatero kenaka adayitana. “Daling’i!”

 

M’chipinda chochezeramo mudalowa msungwana woyerera, wamsinkhu wa pakatikati ndi wonenepera. Adavala bulauzi yothina, pakatipa yosokedwa mwa “v” n’kumaonetsa pokumanirana mawere onga mapapaya. M’chombo udali pamtunda ndipo pamchombopo padakolekedwa ndolo. Thalauza lake lidali lothina ndipo m’chiunomu linkaonetsa panti yemwe adavala. Adavala chipewa cha kepi ngati cha Katakwe koma kepi atayiyang’anitsa m’mbali.

 

Buthuli lidali bwenzi lomwe Katakwe adapeza ku Blantyre. Dzina lake lidali Psa Mbalame ndipo linkagwira ntchito pa bala ija yotchuka ku Ndirande, Club Pa Mbiya.

 

“Kodi ndi alamu a Psa,” adatero Likisho. “Mwatchenatu.”

 

Psa Mbalame adadziyang’ana ndi maso ake akuluakulu anjala ya ndalama. “Za ine umadziwa.”

 

“Aise, inetu ndi bwenzi langali basi ngwa kunyanja,” Katakwe adatero. “Mwina n’kukagwira ntchito m’madzi.”

 

Likisho adadziwa kuti bawo yagona. “Tsono pakhomo pano usiyapo ndani?”

 

“Basi pakhomo mpano nditseka. Kudzatsegula mpa 27 tikabwerako konjoyako.”

 

“Aise, pajatu nthawi ya khrisimasi ndi imene kumachuluka kuba,” Likisho adamuwunikira. “Ndiye sibwino pakhomo kusiyapo popanda munthu.”

 

Katakwe adaseka. Aise, ine ndine shasha. Ndisiya magetsi akuyaka ndiponso wailesi ikulira. Mbava ziziyesa ine ndilipo…”

 

“…apo ife tikubaya mahape kunyanja,” adamaliza Psa Mbalame.

 

“Bwanawe, apolisi amalengeza chaka chilichonse kuti nthawi ya khrisimasi pakhomo osamasiya popanda munthu ndiye…”

 

Katakwe adamudula. “Ndati uike pansi mtima. Ndakuuza kale pulani yanga.”

 

Katakwe ndi Psa adatengana ulendo wokasangalala kunyanja. Uko adanjoyadi. Kumwa. Kuvina. Zonse.

 

Pa 27 December, nthawi ya madzulo adatulukira pakhomo. Katakwe poyamba adaganiza kuti wasokera. Nyumba adafikayo idalibe makatani ndipo pankangowoneka ngati anthu adasamukapo. Koma ayi idali nyumba yake ndithu.

 

Iye adathamangira m’nyumba. M’nyumbamo mudalibe kena kalikonse. Adazindikira kuti adaberedwa kalikonse ndi bulangete lomwe.

 

“Mayo andibera!”

 

“Pajatu anzanu aja adakuwuzani koma inu kusamva,” adamusambira m’manja Psa akutuluka m’nyumbamo. “Inetu ndiye zisandikhudze. Mukalongosola mukudziwa pondipeza- Pa Mbiya”

 

END

 

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *