Katakwe Mavalidwe Mtchalitchi

Katakwe

Mavalidwe Mtchalitchi

Lawrence Kadzitche

 

Zovala sizionetsa khalidwe la munthu. Nthawi zambiri momwe munthu amavalira amangokhala makonda chabe. Komabe ngakhale izi zili chonchi, zovala zili zonse zimakhala ndi malo ake ovalira.

 

Munthu sangapite n’kumakasambira atavala suti kapena kumasewera mpira atavala lilemba. Zovala zimayenerana ndi malo ake.

 

Koma Katakwe atayambitsa tchalitchi yake, ankalola mavalidwe amtundu wina uliwonse mumpingo wakewo. Mulungu sayangana mavalidwe koma mtima, iye ankalalika motero.

 

Motero mavalidwe a m’tchalitchi mwake samasiyana ndi a mu fashion show. Atsikana ankafika atavala masiketi afupi, ena ali m’mathalauza othina aja amati dindadinda. Nawo achinyamata ankafika atakhwefula, mabuluku akungowoneka ngati limachitira thewera la mwana akabibidwa.

 

Zinthu zina zimangokhala bwino kuzikamba. Nkaamba kake pachingerezi pali mwambi woti yemwe akufuna kudya ndi dyabulosi azigwiritsa ntchito sipuni yayitali.

 

Mapemphero a tsikulo adayamba ngati tsiku lina lililonse. Katakwe adali mkati molalika, akuthyola maumfumu ndi maukulu onse a satana, pomwe msungwanayo adalowa.

 

Mwana wamkazi lidali duwa. Kuonjezera apo, Mulungu adamudalitsa mwapadera ndi mawere, mbuyo ndi miyendo. Mawere ake adafuna kuphulitsa komanso kuthawa mbulauzi yake yothina yokhala ndi chidikha chachikulu pamtima. Siketi yomwe adavala idali yayifupi komanso yothina kwambiri.

 

Adalowa akuyenda ngati ali pa catwalk. Nsapato yake yayitali idapanga phokoso. Maso onse adamulondola namwaliyo yemwe adasiya mipando yonse n’kukakhala kutsogolo moyanganana ndi Katakwe.

 

Katakwe adapuma mozama. Ichi chidali chiyani? Mayesero? Adadzilimbitsa mtima kuti awa adali mavalidwe chabe. Koma vuto la maso limakhala lakuti akaona chinthu chochititsa chidwi, amafuna azingochiwona basi.

 

Munthu wa Mulungu adayesa kuthawitsa maso koma adalephera. Msungwanayo ankayika mwendo wina pamwamba paunzake Katakwe akamamuyangana. Katakwe sadakayike kuti amatha kuona kabudula wofiyira yemwe namwaliyo adavala. Bulauzi ya msungwanayo ikasuntha, Katakwe ankatha kuona mikanda yamchiuno.

 

Mwachilungamo, Katakwe sadathe kulalika bwino. Poopa kuyaluka, iye adadula msanga ulaliki n’kulengeza kuti ofuna kupemphereredwa afike kutsogolo. Akadadziwa sadakatero. Palibe adadzuka kupatula mtsikana uja.

 

Nkhawa idamugwira Katakwe. Tsono msungwanayo akagwa ndi mphamvu ya mzimu woyera, zitha bwanji malinga ndi mavalidwe akewo?

 

End

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

8 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *