Katakwe Nthawi Yomweyi Ndalama Yasiya Kuvuta?

Katakwe
Nthawi Yomweyi Ndalama Yasiya Kuvuta?
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Tsikulo mkazi wa Katakwe adali m’tauni. Malinga n’kukwera kwa zinthu, ndalama zomwe adatenga sizidakwanire kugula zinthu zomwe ankafuna. Adamuyimbira Katakwe kuti amuonjezere ndalama zina.

“Make mwana, sindine fakitole yopanga ndalama,” Katakwe adalalata. “Simukudziwa kuti ndalama yavuta? Basi shugayo musagule.”

“Bambo…” adafuna kudandaula mwana wamkazi koma Katakwe adali ataidula foniyo. “Koma azibambo enanso! Tsono akuti ana azikadya bwanji phala lopanda shuga!”

Nthawi yomweyo adangomva, “Gile!”

Potembenuka adaona msungwana yemwe adasamira galimoto yofiyira yamtundu wa VW. Chilichonse pamtsikanayo chidali chooneka chodula. Tsitsi lija amati Brazilian hair lidatuluka m’kachipewa komwe adatsomeka kumutu kwake n’kukagwera m’mapewa. Dilesi lapamwamba lonyezimira lidakuta thupi lake. Kuphazi kudali gogoda yamakono.

“Ndikudziwa kuti wandiyiwala,” namwaliyo adatero. “Ndine Sonia.”

Mkazi wa Katakwe adamukumbukira; adayimbira limodzi sukulu ku pulaimale. “Iii, sindinakuzindikire. Nthawi imene ija udali village girl!”

Sonia adaseka n’kuonetsa mndandanda wamano oyera ngati matalala.
“Panopa I am a town girl.”

“Anzathu zikuoneka kuti zikutheka,” adavomereza mkazi wa Katakwe. “Ndiye ukutani m’tauni muno?”

Msungwanayo adadzitchola. “Basi ndangoyamba nawo chitaka. Ndikukawa azibambo opusa m’tauni muno.”

Mkazi wa Katakwe adaoneka kuti sadatolepo kanthu.

“Ndingoti ndikupanga bizinesi yodyera azibambo-dzina lodyera lake timati ma blesser,” Sonia adanyadira. “Ndimapanga zibwenzi ndi azibambo a dollar basi n’kumatolera kashi kwa iwowo ngati kondakitala.”

“Sonia, moti imeneyo ingakhale bizinesi?”

“Siya, bwanawe; ndiya hot. Panopa pali kamkulu kenakake komwe kafa nane hedi. Ndikamathana nako kakhala kalibe ngakhale wani tambala.”

“Koma nawenso!”

“Mmabanjamutu mukungotayamo nthawi. Yanu ndiyothandiza azibambo kupanga ndalama mpamene yathu ndiyodya kashiyo,” adabwekera Sonia. “Ali pa bo ndani?”

Mkazi wa Katakwe sadathe kuyankha.

“Ndakumva ukuyimbira mwamuna wako kuti akuonjezere ndalama koma wakukanira. Koma ine kuti ndiyimbire blesser wangayo anditumizira pompopompo.”

“Ukunama!”

“Mmayesa ndi amene adandigulira galimotoyi? Ukuti get up ndavalayi adagula ndani?” adanyadira Sonia. “Blesser wake ali loaded bad ndipo kashi yokha nde saumira.”

“Sindikukhulupirira! Alipo amuna ofewa manja choncho?”

“Alipo osati kutali koma ku Malawi konkuno,” Sonia adatero akutulutsa selofoni yapamwamba. “Dikira ndimuyimbire. Honey, ndili pa Shopulaiti. Ndaona dilesi lina lake la bo koma dollar yandiperewera ndiye tabwera udzandipatse. I need five hundred thousand yokha basi.” Adadula foniyo nayikisa. “Akubwera. Uyime chapatali uone zomwe zichitike.”

Mkazi wa Katakwe adakaima chapatali. Sipadapitedi nthawi. Koma iye anadabwa ndi munthu yemwe adatulukira. Adali mwamuna wake Katakwe. Mmanja mudali waleti yodzimbidwa ndi ndalama. Adangofikira kumupatsa Sonia waletiyo. Sonia adasololamo yekha ndalama zomwe ankafuna.

Mwana wamkazi adalephera kuwugwira mtima. Adafika n’kudzaima kumbuyo kwa Katakwe. “Nthawi yomweyi ndalama yasiya kuvuta?”

Katakwe adatembenuka n’kuphana maso ndi mkazi wake. Akadaona mzukwa, mwina adakadabwa mocheperako!

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *