Katakwe- Avala Bulauzi

Katakwe
Avala Bulauzi
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Makamaka m’mizinda ya Lilongwe ndi Blantyre, pali asungwana ena omwe amati kukada, amasamba n’kutchena n’kukaima m’mbali mwa msewu. Iwowa nthawi zambiri amavala mosasiyana n’kukhala maliseche. Motero munthu ukawaona umadziwiratu chomwe aimira m’mbali mwa msewumo.

Iwowatu sadikira anthu oyenda pansi. Amafuna anthu a magalimoto. Galimoto ikamadutsa amaimitsa pokodola kapena powonetsa wina mwa katundu wotsatsira malonda awo monga ntchafu.

N’kumafunsa kuti kodi amatenga asungwana otere amakhala ndani? Amakhala anthu a magalimoto. Ku maofesi amakhala mabwana. Kunyumba amakhala ‘abambo a uje’. Kutchalitchi amakhala akulu ampingo. Koma amadalira mdima kuti zochita zawo zisadziwike.
Katakwe adali bwana pakampani pomwe amagwira ntchito. Kunyumba adali bambo wa ana angapo. Kumpingo adali mtumiki ndipo padali maganizo omusankha mkulu wampingo.

Komatu kukada, ankapita m’tauni n’kukanyamula asungwana oterewa. Kunyumba amangomuwuza mkazi wake kuti achedwa kufika ntchito yachuluka. Akatero amakatenga mmodzi mwa asungwanawo n’kumakachita nawo masewera aja ana amati zopusa ndi mahulewo. Akafika kunyumba kwake, mkazi wake samalotapo kanthu.

Tsikulo, monga mwa masiku onse, Katakwe adatenga msungwana woyima m’mbali mwa msewu. Buthulo lidali mu bulauzi yowoneka ngati gwanda. Katakwe sanachedwe; adatengana ulendo kunyumba yomwe msungwanayo amapangira bizinesi.

Adayiyala nkhani. Ali mkati mocheza, magetsi adazima. Katakwe sanadandaule, pali zinthu zina sizifuna magetsi. Adamaliza kucheza magetsi asadayakebe.

Omwe mudatengako mahule, mukudziwa nyumba zomwe asungwana ozisaka amakhala. Timangokhala timalumu topanda ndi mawindo omwe. Motero ndi kuzima kwa magetsiwo m’chipindacho mudali mdima wonga mtsiro. Koma Katakwe sadafune kudikira kuti magetsi ayake. Akati chiyani kwa mkazi wake akachedwa?

Iye adafufuza zovala zake navala. Adalipira ndalama basi n’kubuthira bwakunyumba. Atafika, adapeza banja lake likuwonera filimu ya Nigeria pa balanza.
Atangolowa anadabwa aliyense akumuyang’ana modabwa. Funso lomwe adati aliponye mkazi wake adafunsa ndi mwana wake wotsiriza.
“Ababa, bwanji mwavala malaya achikazi?”
Katakwe adati dzidzidzi. Adali mu bulauzi ngati Winiko. Heh! Povala malaya mu mdima muja adavala bulauzi ya hule lija!

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *