Katakwe Nyimbo m’tchalitchi

Katakwe

Nyimbo m’tchalitchi

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Chimavuta akhrisitu ambiri chimakhala chiphamaso. Pofuna kuoneka auzimu kwambiri, amabisa zinthu zambiri zomwe amakonda.

 

Chitsanzo chabwino ndi nyimbo. Ambiri opemphera amati samvera nyimbo zomwe sizauzimu pomazitcha kuti ndi zachidziko. Izitu amanena kwa anzawo opemphera kapena akakhala pagulu. Koma umadzapeza anthu omwewo akumvera nyimbozi akakhala okha m’magalimoto kapena m’nyumba.

 

Naye Katakwe, ngakhale adali chiphona pauzimu, ankakonda kwambiri nyimbo zosakhala zauzimu. M’nyumba mwake ankamvera oyimba osiyanasiyana a m’Malawi mommuno ngakhalenso akunja.

 

Paja masiku ano kudabwera mwayi woyika nyimbo yomwe umakonda kuti izilira ukamalandira foni, ringtone pa chingerezi. Katakwe adayika nyimbo ina yake ngati ringtone.

 

Matchalitchi ambiri, abusa amapereka mwayi kuti nthawi zina akulu ampingo azilalikira nawo. Katakwe adali mmodzi mwa akulu ampingo a tchalitchiyo ndipo tsikulo adapatsidwa danga loti alalikire.

 

Adayenda mwa uzimu kupita kuguwa. Uko adatsegula baibulo ndipo adayamba kupantha uthenga. Udalidi uthenga wabwino ndipo ‘alleluya’, ‘amen’, ‘chedwanipo abusa,’ adali ponseponse ngati umboni kuti uthengawo umawafikira anthu moyenera.

 

Poyamba naye anadabwa. “Adandigwira bere, ndili mtulo…” nyimbo idamveka.

 

Katakwe adasiya kulalika. Sadamvetse kuti nyimboyo imachoka kuti. Kenaka adaona maso onse ali pa iyeyo.

 

Apa mpomwe adazindikira. Nyimboyo idali ring tone kapena titi nyimbo yomwe imalira wina akayimba foni yake. Mwana wamwamuna adapisa dzanja mthumba n’kuyidula.

 

Sipadapite nthawi. Woyimba uja adayimbanso. Katakwe adapisanso dzanja kuti angoyizimitsa koma mmalo mwake anadina pokwezera voliyumu ya foniyo. Nyimbo ija ndiye idamveka mokweza.

 

‘Adandigwira bere, ndili mtulo,’ idamveka nyimbo ya Kasambwe Brothers Band. ‘Ndingomva tseketseke, Awidzi abwera…’

 

Thukuta lidatuluka pankhope pa Katakwe. Adaona mafunso pa nkhope pa akhrisitu. Atsogoleri, kani mumamvera nyimbo zachikunja? Pankhope zina ndiye padali mafunso okwiya: nyimbo ngati izi mumakazimvera kuti?

 

End

 

 

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *