Katakwe- Kofunsira Mbeta

Katakwe

Kofunsira Mbeta

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Kofunsira mbeta kumakhala kofunika kusamala. Sikusiyana ndi kofunsira chibwenzi. Munthu umayenera kubisa khalidwe lako lenileni mpaka zonse zitatheka.

 

Pokhala mkoko wogona, a Topitopi amazidziwa zimenezi. “Mphwanga, paja ndiwe wosusuka ndi zakudya,” iwo adamulangiza Katakwe akukonzekera kunyamuka limodzi kupita kokafunsira mbeta. “Kuchilendo zakudya timasiyako ngakhale usadakhute. Wamva?”

 

“Ndikudziwa zimenezo, malume,” Katakwe adavomereza. “Vivian ndi getsi ndipo sindingalore kuti china chake chisokoneze ubwenzi wathu.”

 

“Ndimenyeretu ka morale booster,” a Topitopi adatero akutulutsa kabotolo ka kachasu. “Kofunsa mbeta kumafunika kupita utakweza ti ma bar.”

 

Iwo adanyamuka ulendo wa kwa makolo a Vivian. Kumeneko adapeza makolo komanso malume a namwaliyo akuwadikira. Pokhala anthu amwambo, iwo adati akonze kaye chakudya zokambirana zisadayambe.

 

“Pano ndiye talandiridwa,” adabwekera a Topitopi. “Monga Nthondo adanena, pano mpathu n’kulinga utakhuta.”

 

“Mwalasa, tsibweni,” Katakwe adathirira mang’ombe.

 

Kuchokera kuseri adamva mawu akuti, “Ana inu, tathamangitsani nkhuku iyo tiphikire alendo.”

 

Katakwe adanyambita milomo ndi kumezera malovu. “Mwamva, malume? Tilikwira kwiyokwiyo.”

 

Posakhalitsa adamva mdidi kunja kwa nyumbayo. Ana aja ankathamangitsa nkhuku ija. Katakwe adasuzumira kunjako ndipo nthawi yomweyo mtima wake udazama. Pamoyo wake adali asadawoneko nkhuku yodziwa kuthamanga ngati msotiwo. Nkhukuyo idakhumata nalo liwiro ngati kalulu wothawa agalu a liwamba.

 

Ndi mmene imathawira nkhukuyo, Katakwe adaona kuti anawo sakwanitsa kugwira chiwetocho. Adatha kuona akudyera mnkhwani. Pamenepo sadaganizenso ndi bongo koma nkhuli. Monga msampha, iye adafwamphuka n’kuyamba kuthamangitsa nawo nkhukuyo. Posakhalitsa Katakwe adawadutsa anawo iye n’kukhala patsogolo.

 

Katakwe sadadziwe kuti anawo ankathamangitsira nkhukuyo komwe kudayima apongozi ake akazi kuti mayiwo ndi amene ayigwire. Maso ali pankhukuyo, iye sadawaone apongozi akewo. Nkhuku ija idauluka ndipo nayenso Katakwe adauluka ngati golokipa.

 

“Ndakugwira,” iye adakuwa kwinaku akukagwa limodzi ndi chomwe ankaganiza kuti idali nkhukuyo. Koma anadabwa kuona nkhuku ija ikuwulukira kunja kwa mpanda.

 

Potsitsa maso, Katakwe adaona kuti adawakha mutu wa apongozi ake. A Topitopi, omwe adayima m’khomo lanyumba, adamuyang’ana akupukusa mutu. Adamukodola kuonetsa kuti zinthu zavuta azipita.

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *