Katakwe Msolo wa mbala

Katakwe

Msolo wa mbala

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Kalekale padali munthu wina yemwe adakacheza kwa mzake. Ali kwa mzakeyo, adakhumbira chigwinjiri. Polephera kupirira, adatola chigwinjiricho nkuchiponya mthumba. Adatsanzika, mzakeyo osadziwawapo kanthu.

 

Mbavayo itapita, mpomwe mzake uja adatulukira kuti chigwinjiri chake chasowa. Pakuti padalibe wina aliyense amene adafika pakhomopo, mwini khomoyo adaganiza kuti mwina mzake uja adatengako chigwinjiricho mwangozi.

 

Adamuthamangira mzakeyo. Atamufunsa, wakubayo adakana kuti sadatenge chigwinjiricho. Uja adakhulupirira. Akusiyana, ndipsi ija poyenda, chigwinjiri chija chidaombana ndi makiyi omwe adali mthumbamo ndipo chidalira. Atamusecha, adachipeza mthumbamo.

 

Phunziro lamwambiwu, omwe umati chigwinjiri maliralira chidalira msolo wa mbala, ndilakuti padziko pano palibe chinsinsi. Munthu umatha kumapanga zinthu zamseri koma kamene kamadzakuulura kamakhala komwe sumakaganizira.

 

Katakwe adali ndi khalidwe lonunkha lokonda kumagona ndi mahule. Uhule ndi bizinesi ndipo chomwe mahule amafuna ndi ndalama. Vuto la Katakwe lidali lakuti amasokoneza bizinesi ya mahulewo. Iye ankavuta kwambiri kulipira akagona ndi mahulewo.

 

Mkazi wake samadziwapo kena kalaikonse. Akafika pakhomo, Katakwe amanamizira ngati bambo waulemu wake. Kutchalitchi adali ndi udindo ndipo kuntchito adali bwana waudindo wake.

 

Mwina khalidwe lake lachisembwere siladakaululika adakakhala kuti kampani yomwe amagwirako ntchito siyidakonze phwandolo. Katakwe adaitanidwa kuphwandoko limodzi ndi mkazi wake.

 

Uko adapitiradi limodzi. Chosadziwa, limodzi mwa mahule omwe Katakwe adagonapo nalo lidafika kuphwandoko ndi mkulu wina woyaluka wapakampanipo. Hulelo lidamuona Katakwe koma iye sadalione.

 

Hulelo lidaganiza kuti Katakwe wafika ndi hule lina. Motero, Katakwe atapita kuchimbudzi kukataya madzi, hulelo lidapita pomwe padali mkazi wa Katakwe.

 

Sisi, ndikuona mukuchita khoba ndi mkulu muli nayeyu, lidatero hulelo. Ndiye ndati ndikuchenjezeni; mulandiliretu.

 

Mkazi wa Katakwe anadabwa. Ndilandiliretu?

 

Eya, ambere chire. Mkulu ameneyu amavuta kulipira, hulelo lidafotokoza. Ine ndidagonapo naye, ndidachita kumulanda buluku kuti andilipire.

 

Katakwe akubwerera, ataona mkazi wakeyo ali ndi hule lija, adadziwiratu kuti zinthu zavuta!

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

6 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *