MAI BUSA, MUKHALATU PAMITALA

Katakwe

MAI BUSA, MUKHALATU PAMITALA

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Katakwe adatulukira pakhomo pa mbusayo limodzi ndi mchemwali wake. Mmanja mudali pwitika wonola bwino.

 

“Ali kuti mwamuna wako yemwe amadzitcha kuti mbusayo?” adafunsa Katakwe, chikwanje chija chikuthwanima mdzuwa lamasana amenewo.

 

“Achimwene, pakhomo safika choncho,” mkazi wa mbusayo adamulangiza. “Lowani mnyumba.”

 

Katakwe adalemba pakhonde pa nyumbayo ndi supada uja. Malawi amoto adaoneka ngati moto wamakala.

 

“Sindinabwere kudzacheza,” adakana kulowa Katakwe. “Muuze galu and yemwe umati ndi mwamuna wako abwere panja pompano kapena pakhomo pano patuluka magazi.”

 

Mbusa uja adaonekera mkhomo la nyumbayo. Panthawi ina, Katakwe adakaseka. Mbusayo adali wamfupi ngati chitsa. Adavala suti yamtundu wowala yomwe imaoneka ngati yachikazi ndipo idali ya saizi yaikulu. Tsitsi lake lidali lothira mankwala ndipo ankaonekeratu kuti kuyera kwake kudali kochokera mmafuta oyeretsa. Adavala nsapato yaitali yosongoka yomwe ndi msinkhu wake waufupiwo imangooneka ngati ali pazisudzo.

 

“Ndakulandirani mdzina la ambuye, atsogoleri,” mbusayo adatero mmawu ake ogontha kaamba kokukwa polalika. “Lowani mnyumba.”

 

“Sindinabwere kudzacheza,” Katakwe adabwereza. “Msungwana uyu mukumudziwa?”

 

“Yes, ndikumudziwa,” adavomereza mbusayo. “Timapemphera limodzi.”

 

“Good. Ameneyu ndi mchemwali wanga,” Katakwe adatero. “Mwakhala mukumuuza kuti mwamuna wake siamene Mulungu adamulembera. Zotsatira zake iyeyu amachita zosasamala banja ndipo mwamuna wake wamuthamangitsa,” Katakwe adafotokoza.

 

“Mr. Katakwe…”

 

“Chomwe ndabwerera pano nchakuti mumuuze kuti mwamuna yemwe Mulungu adamulemberayo ndi uti,” Katakwe adamudula mbusayo. “Mukapanda kutero, nde mumukwatira ndinu.”

 

Mkazi wa mbusayo adaona kuti Katakwe samacheza. “Achimwene…”

 

“Mai, amuna anuwa akapanda kupereka dzina la mwamuna yemwe Mulungu adamulembera mchemwali wangayu, ine ndikumusiya pano,” Katakwe adatsimikiza. “Mukhala pa mitala, mai busa.”

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

4 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *