Katakwe Akana kulalikira pamaliro

Katakwe

Akana kulalikira pamaliro

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Nthawi yomwe Katakwe ankaponya khasu lake pa phunzi ndi momwe anthuwo amatulukira.

 

“Abusa kodi mukutalikira?” Mdzibwa adafunsa modabwa akuyang’ana ovolosi yomwe Katakwe adavala.

 

“Ayi, ndupita kudimbaku n’kagauleko pobyala tanaposi.”

 

Anthuwo adayang’anitsitsana.

 

“Pepani, abusa, kodi simudalandire thenga loti Punganyizani wamwalira kucha kwa lero?” adafunsa Gulugusha

 

“Thenga ndalandira ndithu,” adatsimikiza mwachidule Katakwe.

 

Akuluakuluwo adaombetsananso maso.

 

“Abusa, pajatu Punganyizani adali mkhrisitu wanu ndiye timafunatu mukalalike pamaliro pake.”

 

“A Gulugusha, inetu sindingakalalike pamaliro a Punganyizani,” Katakwe adakana.

 

“Abusa, musatero. Chavuta n’chiyani?”

 

“A Gulugusha, mwayiwala momwe malemuwa amanyozera ine komanso mpingo?”

 

“Abusa, baibulo limati munthu woipa tisamubwezere choipa,” adalowererapo a Dalomani omwe adalinso mkulu wampingo.

 

“Atsogoleri, tiyeni apa tikambe chilungamo. Punganyizani ankati chiyani zaine?”

 

“Ndinu a ulesi simufuna kugwira ntchito koma kudyera akhrisitu m’dzina la Yesu.”

 

“Eetu, Punganyizani wakhala akuyesetsa kugwetsa mphwayi akhrisitu kuti asamapereke ndalama ati poti Mulungu sagwiritsa ntchito ndalama. Paja ndinkati ndikamapempha ndalama amati ndufuna kusandutsa mpingo bizinesi?”

 

“Abusa…”

 

“Iye samati bwanji ife azibusa sitigwira ntchito koma kumangodalira kudyetsedwa ndi akhrisitu? Ndiyetu panopa ndikukagwira ntchito yoti ndipeze kangachepe kodyetsa banja langa m’malo momadalira za m’mbale.”

 

Akuluakuluwo adayesetsa kumukhazika mtima pansi Katakwe.

 

“Akhrisitu ambiri mbusa akamakamba za ndalama amakonda kunena kuti ngokonda ndalama. Chomwe amayiwala n’choti mbusa amakhala akulalikira, kuyendera odwala, kulalikira pamaliro, choncho nthawi yogwirira ntchito angayipeze bwanji? Akhristuwo ndiwo ayenera kumusalamalira.”

 

end

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

4 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *