Katakwe-MOTO WAMACHIRITSO

Katakwe
MOTO WAMACHIRITSO
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Ngati pali utumiki womwe umadyetsa bwino ndi utumiki wamachiritso. Munthu akapemphereredwa n’kuchira nthawi zambiri amakathokoza mbusa womupemphererayo ndi mphatso kapena ndalama.
Kuyendetsa utumikiwu sikukhala kovuta. Choyamba, anthu ena omwe amabwera kudzapempheredwa amakhala kuti akupitanso mobisa kuchipatala ngakhale kung’anga kumene. Motero akachira ndi mankhwala achizunguwo kapena achikudawo, wopemphererayo amangoti, male! China, ambiri amakhala ozingwa ngati munthu wokokoleredwa ndi madzi ndipo chili chonse chomwe angauzidwe amangovomera.
Izi Katakwe adazitulukira mwachangu. Motero, adasiya ntchito yake ya uphunzitsi, n’kukakwera phiri masiku angapo, potsika n’kulengeza kuti ambuye amupatsa mphatso yamachiritso. Nthawi zambiri, iye chomwe ankafuna chinkakhala ndalama. Koma atamuona mayi yemwe adafika tsikulo, dyabulosi kachiwanda adamulowa m’njira ina. Ngati mbusa iye ankaona akazi okongola, koma mayiyo zidali zina. Adali ngati duwa loti langomasula kumene ndipo iye adatengeka monga njuchi yoti yathira diso pa duwalo.
“Bobobo khethekhethe shakalala mandelele bobobo khekhethe,” Katakwe adaombeza mu uzimu. “Mayi, mukudwala chifukwa muli ndi chiwanda choyipa kwambiri chofunika kupemphera masiku asanu kuti chituluke.”
Mayiyo adavomera. Adali ndani kuti atsutse m’busa?
“Ndiye mayi, ndizikuyenderani ndine kunyumba kwanu kudzakupemphererani,” iye adatero. “Ndintchito yathu ife abusa kutumikira nkhosa.”
Katakwe adayamba kumapita kunyumba kwa mayiyo kukamupempherera. Iye ankawonetsetsa kuti akufika pakhomopo nthawi yomwe mwamuna wamayiyo adali kuntchito.
“Koma mukuona kusintha?” adafunsa Katakwe tsiku lachitatu.
“Ayi, abusa,” adayankha mwana wamkazi mwachilungamo.
“Mashalakhatha sikwenta metikashi khethekhethe! Paja ndidakuwuzani kuti muli ndi chiwanda chankhakamira,” Katakwe adalongosola. “Chiwanda chokwiya chimafunika mapemphero okwiyanso. Ndikukumbatirani; moto wamachiritso uzichoka m’thupi mwangamu kulowa mwa inuyo.”
Mayiyo adavomera. Adali ndani kuti atsutse zonena za wodzozedwa wa Yehova? Katakwe adamukumbatira. “Mayi, mukuumva moto?”
“Kuchokera kuti?” mwana wa mkazi adafunsa.
“M’thupi mwangamu,” adayankha Katakwe.
“Ayi.”
Katakwe adanyambita milomo yake ndi kumezera malovu. “Ndiye kuti sindinakukumbatireni bwino. Vinti sinku sikwenta manderere, inuyo muyenera kumva moto kuchokera m’thupi mwangamu. Umenewo ukhala moto wamachiritso.”
Mayiyo sadafune kunama. “Ayi, sindikumva kalikonse.”
Katakwe adamukumbatira mayiyo ngati nyani kumimba kwa make. Pankhope pake padalibe chisomo ngakhale pang’ono. Iye adapemphera m’chilankhulo chosamveka kenaka adati, “Ambuye andiuza kuti moto wamachiritso ukutsakamira m’zovala zathu.”
Tsikulo zidangochitika kuti mwamuna wamayiyo adaganiza zobwerera kunyumba kuti akaone kuti mapemphero opempherera mkazi wake amayenda bwanji. Adalowera chitseko chakuseri.
“Libo tchakalala mandelele minya bonita sinyorita khethekhethe libobobo venya aki,” Katakwe adapitirira kupemphera osadziwa kuti mwamuna wamkaziyo wafika. Kenaka adatanthauza, “Ambuye akuti tivule zovala zathu zonse kuti moto usamaime penapaliponse. Dondodondo bobo khelekethe; ndiziyendetsa manja anga pathupi panu kuti moto wamachiritso uyake bwino.”
Katakwe adaona chikayiko pankhope yamunthu wamayi. “Bobobobo dododo khethethethe mulere bonita,” iye adapepemphera akudzigwedeza ngati nkhuku ikamakutumula madzi kuchokera m’nthenga zake. “Mayi, musatsutse zofuna za mzimu woyera….”
Sadamalize kulankhula chifukwa adapeza akutembenuzidwa ndi mwamuna wamkaziyo ndipo chibakera chokungidwa bwino chili pasipidi kulondola nkhope yake!
End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

6 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *