Katakwe AGWA CHAGADA

Katakwe
AGWA CHAGADA
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Chimasomaso n’choipa. Chimadetsa m’maso. Katakwe adali paulendo wochokera ku Blantyre kupita ku Lunzu. Koma atamuona msungwana yemwe adayima pasiteji ya pa Chileka Round About mtima wake udadumpha popanda dzenje muja amachitira chule.

Ngakhale pasitejipo padali anthu ambiri, msungwanayo adawala ngati duwa pakati patchire. Mwana wamkazi lidali gesti. Mawere a njo adafuna kuphulitsa bulauzi yake yothina pomwe buluku lomwe lidamukwana ngati sitonkeni lidaumba bwino mbuyo yosafuna mbereko pobereka mwana. Kumutu adatsomekako kachipewa kakuda.

Katakwe adaponda buleki. Anthu omwe adali pasitejipo adathamangira galimotoyo. Katakwe adawabweza pokupiza dzanja lake. Adamukodola msungwana uja. Mwana wamkazi adafika monyada.

“Wakuti, chemwali?”

“Ndikupita pa Zalewa Turn Off,” adayankha munthu wamayi.

Katakwe adadya mutu mwachangu. Iye ankapita ku Lunzu ndipo pa Lunzu padali pafupi kwambiri. Kuti amutenge mtsikanayo n’kukamutsita pa Lunzu sadakakhala ndi nthawi yokwanira yoti acheze ndi duwalo. Motero adaganiza zonama kuti naye akupita ku Zalewa. Kuti adutse Matindi, Lirangwe, Mdeka mpaka kukafika pa Zalewa Road Block padali mtunda. Sadakayike kuti mmene azikafika, apeza danga lolankhula mawu a kukhosi.

Katakwe adaonetsa dzino. “Kwerani, sisi; simulipira poti nanenso ndikupita ku Zalewa komweko.”

“Zikomo kwambiri, bambo,” msungwanayo adadukiza nayitana mwamuna yemwe adayima chapafupi. “Amuna anga, tiyeni. Achimwenewa akuti akupita ku Zalewa.”

Mtima wa Katakwe udadumpha. Mkaziyo adalinso ndi mwamuna wake? Apanga bwanji?

Adakaganiza izi, mwamuna wa mkaziyo adalowa m’galimotomo n’kukhala mpando wakutsogolo. Msungwanayo adakhala mpando wakumbuyo.

Katakwe adavutika mumtima. Atani? Asintha bwanji? Adali atanena kale kuti akupita ku Zalewa. Kuti asinthe ndiye kuti zidziwika kuti adali ndi maganizo ofuna kufunsira buthulo. Motero adayenera kupitabe. Koma funso: mwamuna wa mkaziyo ali m’galimotomo, atulutsa bwanji mawu akukhosi? Mwatsoka, msungwanayo adali asadamufunse nambala yake ya foni ngakhale dzina lake kumene. Apa, monga nyani uja wa ichi chakoma, adali atagwa chagada!

Kuchoka ku Blantyre kukafika ku Zalewa ndi mtunda woposa makilomita makumi asanu. Katakwe adatha mtunda wonsewu popanda kutulutsa mawu ngati bububu kwinaku atalunda ngati mwana waumbombo. Atamutsitsa msungwanayo ndi mkazi wake pa Zalewa, ulendo wobwerera ku Lunzu udamutalikira kwambiri!

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

4 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *