Katakwe KODI TIZIKHALA CHONCHO

Katakwe

KODI TIZIKHALA CHONCHO?

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

M’banja lawolo mudali ana asanu. Onse adali pantchito zabwino. Pokhala wachisamba, Katakwe ndi amene adalandira uthengawo. Adatumiza ndi a Topitopi.

 

“Kuno mayi anu a Namnyama atisiya,” adatero a Topitopi pa lamyayo.

 

Kuchuluka nkwabwino. Ngakhale kumatha ndiwo koma zinthu zimayenda mosavuta. Atalandira uthengawo, onse adalumikizana ndipo adagwirizana zofunika kuchita. Katakwe adati agula bokosi. Wina adati apereka mayendedwe. Ena adati agula zakudya.

 

Onse adanyamuka mmagalimoto awo apamwamba limodzi ndi maanja awo. Monga mmene zimakhalira kukachitika maliro, iwo adaperekezedwa ndi anzawo ambiri akuntchito komanso omwe amakhala nawo.

 

Mu mbiri ya mudzi wa Katakwe, kudali kusadasonkhaneko magalimoto ochuluka ngati omwe adafikawo. Koma chomvetsa chisoni chidali choti kuona nyumba yomwe ankati mudali maliro, munthu sadakakhulupirira kuti adali ndi ndi ana opeza bwino choncho. Idali yamaudzu ndipo mang’alu adali paliponse. Ganizo la aliyense woyiwona kumene lidali loti lidali bwinja loti anthu adasamukamo.

 

Atafika, adapeza a Topitopi akudikira panja pabwinjalo. Panjapo adayikapo tebulo. A Topitopi adalamula kuti bokosi lisalowe mnyumba koma liyikidwe patebulopo.

 

“Ndathokoza chifukwa chakufika kwanu,” a Topitopi adalengeza. “Panopa ndipereka mpata kwa kuti tione omwe atisonkhanitsa pano.”

 

Monga mzukwa, anthu anadabwa a Namnyama akutulukira. Munthu wamayi adali mafupa okolekerapo nsanza. Sipadalinso pochita kufotokoza kuti mayiwo adali owonda chifukwa chosowa zakudya komanso kuti adali pa umphawi wadzaoneni.

 

“Awawa ndiye mayi a ana abwera pano pamagalimoto odulawa,” a Topitopi adaunikira. “Tonse tikhoza kuona kuti ali paulombo woipa komanso akusowa zakudya ngati galu wopanda khomo.”

 

Maso a onse adamatitira pa mayi Namnyama.

 

A Topitopi adapitirira kulankhula. “Mayiwa akhala akudwala, kutumiza uthenga kwa ana awowa palibe yemwe amawatumizira chithandizo. Nthawi zambiri amagona ndi njala, akati adya ndiye kuti wina wachifundo pamudzi pano wawapatsako chakudya.”

 

Maso a anthu adapita pa Katakwe ndi abale ake.

 

“Kuwapempha thandizo anawa, palibe ndi mmodzi yemwe amene amatumiza olo kubwera kuti adzawaone,” a Topitopit adapitirira. “Ndiye n’taona zafika poyipa mpomwe ndinangoganiza kuti nditumize uthenga woti amwalira.”

 

Katakwe ndi abale ake adangoti khuma ngati nkhuku zachitopa. “Zimenezi anthu timazikonda. Munthu timamusiya azivutika koma akamwalira ndiye kuthandiza. Ndidakapanda kunamizira maliro palibe ndi mmodzi yemwe pa anawa adakabwera. Kodi tizikhala choncho?”

 

end

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *