Tsiku La Fote

 

Katakwe
TSIKU LA FOTE
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Kaya zidachokera pati koma pa chichewa pali mawu omwe amati tsiku lafote limakwana. Mawuwa amatanthauza kuti munthu ukamachita zachinyengo pakhalekhale tsiku lina umadzagwidwa.

Katakwe ankaona kuti adazisanja bwino ngati njerwa panyumba yomangidwa bwino. Nomsa ankakhala ku Lilongwe pomwe Steria ankakhala ku Blantyre. Onsewa adali zibwenzi zake ndipo kwa iye ankaona kuti padalibe njira yomwe iwowa adakadzadziwirana. Pofuna kuonetsetsa kuti chinsinsi chake chidali chokungana ngati chibakera, iye sankalola kupatsa asungwanawo zithunzi zake. Komanso sadalinso pa masamba a mchezo ena aliwonse.

Nthawi zonse Katakwe ndi amene ankapita kukamuchezera Nomsa motero iye adalibe nkhawa yoti asungwana awiriwo akhoza kudzabampana. Komanso onsewo adawauza maina osiyana. Kwa Nomsa adali Abruzi pomwe kwa Steria adali Samora.

“Ndidazisanja bo ngati nyumba ya upstairs,” iye adanyadira kwa mzake Likisho. “Nomsa ku bwaila akungoti alipo yekha aponso Steria ku kabula kuno akungoti alipo yekha. Asungwana amenewa akumana ndi player.”

Nthawi idapita Katakwe akuyendetsa zibwenzi zake motere.

“Bae, wiki yamawa ndibwera ndidzacheze,” Nomsa adatero tsiku lina. “Ndibwera Saturday.”

“You will be so welcome, my darling,” Katakwe adavomera.

Poopa kuti mwina Nomsa akhoza kudzakumana ndi Steria, iye adamunamiza Steria kuti akuchokapo akupita kumsonkhano ku Salima. “Weekend ino sindikhalapo.”

“Nde zakhala bho,” adatero Steria. “Nanenso pali mzanga winanso akubwera nde ndikamulandira ameneyo.”

Tsiku loweruka, Katakwe adapita ku depoti ya basi kukamulandira Nomsa. Akufika anadabwa kuona Steria alinso padepotipo. Pokhala kathyali, iye adanama kuti ulendo uja udalephereka. Asadafotokoze kuti wadzatani, basi idafika ndipo Nomsa adatsika. Msungwana adathamanga n’kudzahaga Katakwe kenaka n’kudzambatiranso Steria.

Maso a Katakwe adatuzuka ndi kudabwa. Kukamwa kudatsekuka ndi kutsekeka ngati kwa chambo chovuulidwa mmadzi. Chimachitika n’chiyani?

“Steria, meet my boo, Abruzi,” adapereka ma introduction Nomsa. “Abruzi, meet my best friend Steria.”

Katakwe adadziwiratu kuti tsiku la fote amanena lija ndilimeneli.

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

8 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *