Amayi Amasiye

Katakwe
AMAYI AMASIYE
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Nkhani yake idali motere. Udali umodzi mwa mipingo yomweyi yopanda adilesi. Katakwe ndi amene adayambitsa mpingowo ndipo ndiyemwenso adali mbusa wamkulu wa mpingowo. Father and founder, pachingerezi matero.

Ngati mbali imodzi ya utumiki, mpingowo unkathandiza amayi amasiye ndi zinthu zosiyanasiyana monga zovala ndi zakudya. Zambiri mwa izi zinkhala zochokera kwa anthu akufuna kwabwino omwe ankamupatsa Katakwe kuti azithandizira amayi amasiyewo.

Kaamba kakhama lomwe mbusa Katakwe amaonetsa pantchitoyi, utumikiwu udakula ndipo anthu ambiri adayamba kuthandiza pautumikiwo. Zonse zidali bwino ndithu mpaka pomwe padayamba kumveka mphekesera zakuti Katakwe amagonanso ndi amayiwo.

Podziwa kuti utsi sufuka popanda moto, akulu ampingo nkhaniyi itawapeza adaganiza zokhala pansi ndi mbusa wawoyo. Adayiyambitsa nkhani adali Josofati, mtsogoleri wa Church Council.

“Pepani abusa, kodi nkhani tikumvayi ndiyowona?”

Pomwe onse ankaganiza kuti munthu wa Mulunguyo akana, anadabwa iye akuvomera. “Eya ndiyowona,” Katakwe adavomera thima liri ziii.

Padapita kanthawi atsogoleriwo akugaya yankho lomwe adalandiralo. “Abusa, utumiki wanu ukupita patsogolo chifukwa chantchito yabwino yomwe mukugwira kuthandiza amayi amasiye, ndiye mukufuna muononge ntchito yonseyi chifukwa cha dama?”

Katakwe adamwetulira. “Sindikuononga ntchito koma kupititsa patsogolo ntchitoyo.”

Apa akulu ampingo aja adatinso jenkha.

“Zofuna za amayi amasiye sizovala ndi zakudya zokha,” adapitiriza Katakwe. “Amafunanso zinthu zina monga kukhala pamodzi ndi mwamuna. Tsopano iwowa mwamunayo alibe, mumati azikhala ndi ndani?”

Palibe adayankha.

“Chabwino, ine ndisiya,” adadzipereka mbusa Katakwe. “Ndiye pakati panupa ndani amene alowe mmalo mwanga kuthandiza mayiwa kuzofuna zawo zathupi?”

Palibe adakweza dzanja.

“Naye mayi wamasiye ndimunthu ndipo amakhala ndi zilakolako motero ine ngati mbusa wawo ndiyenera kupeza njira yowathandizira,” adatsendera Katakwe. “Ndimachitazi ndi mbali imodzi yautumiki yowonetsetsa kuti amayi amasiye amumpingo uno sakusowa kanthu kuthupi komanso kuuzimu. Kulakwa kwanga kuli pati pamenepo?”

End.

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

10 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *